Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 4:27 - Buku Lopatulika

27 nakagona ndi kuuka, usiku ndi usana, ndipo mbeu zikamera, ndi kukula, iye sadziwa umo zichitira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 nakagona ndi kuuka, usiku ndi usana, ndipo mbeu zikamera, ndi kukula, iye sadziwa umo zichitira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Iyeyo atha kumangogona usiku, m'maŵa nadzuka, nthaŵi yonseyo mbeu adafesa zija zikumera ndi kukula, mwiniwakeyo osadziŵa m'mene zonsezi zikuchitikira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Usiku ndi usana, kaya agona kapena adzuka, mbewu imamera ndi kukula, ngakhale sadziwa mmene zimachitikira.

Onani mutuwo Koperani




Marko 4:27
8 Mawu Ofanana  

Monga sudziwa njira ya mphepo, ngakhale makulidwe a mafupa m'mimba ya mkazi ali ndi pakati; momwemo sudziwa ntchito za Mulungu amene achita zonse.


pamenepo ndinaona ntchito zonse za Mulungu kuti anthu sangalondole ntchito zichitidwa pansi pano; pakuti angakhale munthu ayesetsa kuzifunafuna koma sadzazipeza; indetu ngakhalenso wanzeru akati, ndidziwa, koma adzalephera kuzilondola.


Ndipo ananena, Ufumu wa Mulungu uli wotero, monga ngati munthu akataya mbeu panthaka;


Nthaka ibala zipatso zake yokha; uyamba mmera, zitsata ngala, pamenepo maso okhwima m'ngalamo.


Tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera; pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake;


Koma kulani m'chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu; kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa