Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 4:28 - Buku Lopatulika

28 Nthaka ibala zipatso zake yokha; uyamba mmera, zitsata ngala, pamenepo maso okhwima m'ngalamo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Nthaka ibala zipatso zake yokha; uyamba mmera, zitsata ngala, pamenepo maso okhwima m'ngalamo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Paja nthaka imabereketsa mbeuzo yokhayokha. Umayamba ndi mmera, kenaka ngala, pambuyo pake njere m'ngala muja zimakhwima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Nthaka pa yokha imatulutsa mbewu, umayamba mʼmera, kenaka ngala, kenaka mbewu yokhwima mʼngalayo.

Onani mutuwo Koperani




Marko 4:28
19 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova Mulungu anameretsa m'nthaka mitengo yonse yokoma m'maso ndi yabwino kudya; ndiponso mtengo wa moyo pakati pamundapo, ndi mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa.


Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.


Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.


Kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake;


Chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m'mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.


Pakuti monga dziko liphukitsa mphundu zake, ndi monga munda umeretsa zobzalamo, momwemo Ambuye Yehova adzaphukitsa chilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse.


Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kutuluka kwake kwakonzekeratu ngati matanda kucha; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko.


Koma pamene mmera unakula, nubala chipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole.


nakagona ndi kuuka, usiku ndi usana, ndipo mbeu zikamera, ndi kukula, iye sadziwa umo zichitira.


Pakucha zipatso, pamenepo atenga chisenga, pakuti nthawi yakumweta yafika.


pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;


kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa