Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 3:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo anamuyang'anira Iye, ngati adzamchiritsa tsiku la Sabata; kuti ammange mlandu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo anamuyang'anira Iye, ngati adzamchiritsa tsiku la Sabata; kuti ammange mlandu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Anthu ena ankafuna chifukwa choti akamnenezere Yesuyo, motero ankangomuyang'anitsitsa kuti aone ngati achiritse munthuyo pa tsiku la Sabata.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ena a iwo anafunafuna chifukwa chakuti akamuneneze Yesu, potero anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angamuchiritse tsiku la Sabata.

Onani mutuwo Koperani




Marko 3:2
12 Mawu Ofanana  

Woipa aunguza wolungama, nafuna kumupha.


Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzampambana iye, ndipo tidzambwezera chilango.


Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola chifukwa Daniele, kunena za ufumuwo; koma sanakhoze kupeza chifukwa kapena cholakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo saonana chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye.


ndipo onani, munali munthu wa dzanja lopuwala. Ndipo anamfunsitsa Iye, ndi kuti, Nkuloleka kodi kuchiritsa tsiku la Sabata? Kuti ampalamulitse mlandu.


Ndipo ananena ndi munthu ali ndi dzanja lopuwala, Taimirira pakati.


Ndipo panali pamene Iye analowa m'nyumba ya mmodzi wa akulu a Afarisi tsiku la Sabata, kukadya, iwo analikumzonda Iye.


Ndipo anamyang'anira, natumiza ozonda, amene anadzionetsera ngati olungama mtima, kuti akamkole pa mau ake, kotero kuti akampereke Iye ku ukulu ndi ulamuliro wa kazembe.


Ndipo alembi ndi Afarisi analikumzonda Iye, ngati adzachiritsa tsiku la Sabata; kuti akapeze chomneneza Iye.


Koma ichi ananena kuti amuyese Iye, kuti akhale nacho chomneneza Iye. Koma Yesu, m'mene adawerama pansi analemba pansi ndi chala chake.


Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sachokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zizindikiro zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa