Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 13:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo pamene adzapita nanu kumlandu, nadzakuperekani, musade nkhawa usanayambe mlandu ndi chimene mudzalankhula; koma chimene chidzapatsidwa kwa inu m'mphindi yomweyo, muchilankhule; pakuti olankhula si ndinu, koma Mzimu Woyera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo pamene adzapita nanu kumlandu, nadzakuperekani, musade nkhawa usanayambe mlandu ndi chimene mudzalankhula; koma chimene chidzapatsidwa kwa inu m'mphindi yomweyo, muchilankhule; pakuti olankhula si ndinu, koma Mzimu Woyera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsono akadzakugwirani ndi kukuperekani ku mlandu, musadzaderetu nkhaŵa nkumaganiza kuti, ‘Kodi tikanene chiyani?’ Ai, inu mukangonena zimene Mulungu akakuuzeni pa nthaŵi imeneyo. Pajatu odzalankhula sindinu ai, koma Mzimu Woyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Nthawi iliyonse pamene mwamangidwa ndi kuyimbidwa mlandu, musadandaule za zimene mudzanena. Zimene mudzapatsidwe pa nthawiyo yankhulani; pakuti sindinu amene mudzayankhula, koma Mzimu Woyera.

Onani mutuwo Koperani




Marko 13:11
25 Mawu Ofanana  

Mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine, ndi mau ake anali pa lilime langa.


Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi m'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.


Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu ku bwalo la akulu a milandu, nadzakukwapulani inu m'masunagoge mwao;


Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuti amuphe, ndi atate mwana wake; ndi ana adzayambana ndi akuwabala, nadzawaphetsa.


Koma inu mudziyang'anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu ku bwalo la akulu a milandu; ndipo adzakukwapulani m'masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafumu mudzaimirira chifukwa cha Ine, kukhale umboni kwa iwo.


Koma zisanachitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, chifukwa cha dzina langa.


Yohane anayankha nati, Munthu sangathe kulandira kanthu, ngati sikapatsidwa kwa iye kuchokera Kumwamba.


Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.


Mulungu wa Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wake Yesu; amene inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula.


Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.


Ndipo sanathe kuipambana nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye.


Ndipo anampenyetsetsa onse akukhala m'bwalo la akulu a milandu, naona nkhope yake ngati nkhope ya mngelo.


Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira padzanja lamanja la Mulungu,


Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu.


chimene sanachizindikiritse ana a anthu m'mibadwo ina, monga anachivumbulutsa tsopano kwa atumwi ndi aneneri ake oyera mwa Mzimu,


Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.


Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikire iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa