Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 10:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo anati, Mose analola kulembera kalata yachilekaniro, ndi kumchotsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo anati, Mose analola kulembera kalata wakulekanira, ndi kumchotsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Iwo adati, “Mose adalola kuti munthu azilembera mkazi wake kalata yachisudzulo kenaka nkumuchotsa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Iwo anati, “Mose amaloleza mwamuna kulemba kalata ya chisudzulo ndi kumuchotsa mkazi.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 10:4
7 Mawu Ofanana  

Atero Yehova, Kalata ya chilekaniro cha amai ako ali kuti amene ndinamsudzula naye? Pena ndani wa angongole anga amene ndamgulitsa iwe? Taona chifukwa cha zoipa zanu munagulitsidwa, ndi chifukwa cha kulakwa kwanu amanu anachotsedwa.


Amati, Ngati mwamuna achotsa mkazi wake, ndipo amchokera iye, nakhala mkazi wa wina, kodi adzabweranso kwa mkaziyo? Dzikolo kodi silidzaipitsidwa? Koma iwe wachita dama ndi mabwenzi ambiri; koma bweranso kwa Ine, ati Yehova.


Koma Yosefe, mwamuna wake, anali wolungama, ndiponso sanafune kunyazitsa iye, nayesa m'mtima kumleka iye m'tseri.


Iwo ananena kwa Iye, Nanga chifukwa ninji Mose analamula kupatsa kalata yachilekaniro, ndi kumchotsa?


Ndipo Iye anayankha nati kwa iwo, Kodi Mose anakulamulani chiyani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa