Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 10:32 - Buku Lopatulika

32 Ndipo iwo anali m'njira alinkukwera kunka ku Yerusalemu; ndipo Yesu analikuwatsogolera; ndipo iwo anazizwa; ndipo akumtsatawo anachita mantha. Ndipo Iye anatenganso khumi ndi awiriwo, nayamba kuwauza zinthu zimene zidzamfikira Iye,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Ndipo iwo anali m'njira alinkukwera kunka ku Yerusalemu; ndipo Yesu analikuwatsogolera; ndipo iwo anazizwa; ndipo akumtsatawo anachita mantha. Ndipo Iye anatenganso khumi ndi awiriwo, nayamba kuwauza zinthu zimene zidzamfikira Iye,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Pamene iwo anali pa ulendo wopita ku Yerusalemu, Yesu ankayenda patsogolo pa ophunzira ake. Ophunzirawo anali oda nkhaŵa kwambiri. Ndipo anthu amene ankaŵatsatira anali ndi mantha. Yesu adaŵaitaniranso pambali ophunzira khumi ndi aŵiri aja, nayamba kuŵafotokozera zimene zinalikudzamugwera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Ali pa ulendo wawo wopita ku Yerusalemu, Yesu ali patsogolo, ophunzira ake anadabwa, ndipo amene amamutsatira amachita mantha. Anatenganso ophunzira ake khumi ndi awiri pa mbali ndipo anawawuza zimene zikamuchitikire Iye.

Onani mutuwo Koperani




Marko 10:32
12 Mawu Ofanana  

Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo chizindikiro; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira.


Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda:


Ndipo Iye anayankha nati, Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwe kwa iwo.


Ndipo anazizwa onse, kotero kuti anafunsana mwa iwo okha, kuti, Ichi nchiyani? Chiphunzitso chatsopano! Ndi mphamvu alamula ingakhale mizimu yonyansa, ndipo imvera Iye.


ndipo sanalankhule nao wopanda fanizo: koma m'tseri anatanthauzira zonse kwa ophunzira ake.


Ndipo m'mene anapotolokera kwa ophunzira ake, ali pa okha, anati, Odala masowo akuona zimene muona.


Ndipo m'mene adanena izi anawatsogolera nakwera ku Yerusalemu.


Ndipo panali, pamene anayamba kukwanira masiku akuti alandiridwe Iye kumwamba, Yesu anatsimikiza kuloza nkhope yake kunka ku Yerusalemu,


Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, anati kwa ophunzira anzake, Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi.


Ophunzira ananena ndi Iye, Rabi, Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo munkanso komweko kodi?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa