Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 10:33 - Buku Lopatulika

33 nati, Taonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi; ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka Iye kwa anthu a mitundu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 nati, Taonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi; ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka Iye kwa anthu a mitundu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Adati, “Tilitu pa ulendo wa ku Yerusalemu. Kumeneko Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Iwo akamuweruza ndi kugamula kuti aphedwe. Ndipo akampereka kwa anthu akunja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Iye anati, “Ife tikupita ku Yerusalemu ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo. Adzamuweruza kuti aphedwe ndipo adzamupereka kwa anthu a mitundu ina,

Onani mutuwo Koperani




Marko 10:33
23 Mawu Ofanana  

Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.


Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.


muganiza bwanji? Iwo anayankha nati, Ali woyenera kumupha.


ndipo anammanga Iye, namuka naye, nampereka Iye kwa Pilato kazembeyo.


Mwamva mwano wake; muyesa bwanji? Ndipo onse anamtsutsa Iye kuti ayenera kufa.


Ndipo pomwepo mamawa anakhala upo ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, ndi alembi, ndi akulu a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato.


Ndipo anayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kuti Mwana wa Munthu akamve zowawa zambiri, nakakanidwe ndi akulu ndi ansembe aakulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo mkucha wake akauke.


Ndipo Iye ananena nao, Eliya ayamba kudza ndithu, nadzakonza zinthu zonse; ndipo kwalembedwa bwanji za Mwana wa Munthu, kuti ayenera kumva zowawa zambiri ndi kuyesedwa chabe?


Pakuti anaphunzitsa ophunzira ake, nanena nao, kuti, Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja anthu, ndipo adzamupha Iye; ndipo ataphedwa, adzauka pofika masiku atatu.


koma iwo anafuula, nanena, Mpachikeni, mpachikeni pamtanda.


nati, Kuyenera kuti Mwana wa Munthu amve zowawa zambiri, ndi kukanidwa ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi, ndi kuphedwa, ndi kuuka tsiku lachitatu.


Pamenepo anamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowe ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paska.


kuti mau a Yesu akwaniridwe, amene ananena akuzindikiritsa imfa imene akuti adzafa nayo.


Yesu anamyankha iye, Simukadakhala nao ulamuliro uliwonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera Kumwamba; chifukwa cha ichi iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo tchimo loposa.


Pakuti iwo akukhala mu Yerusalemu, ndi akulu ao, popeza sanamzindikire Iye, ngakhale mau a aneneri owerengedwa masabata onse, anawakwaniritsa pakumtsutsa.


Ndipo, taonani, ndipita ku Yerusalemu womangidwa mumzimu, wosadziwa zimene zidzandigwera ine kumeneko;


Munamtsutsa, munapha wolungamayo, iye sakaniza inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa