Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 1:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo pomwepo anawaitana: ndipo anasiya atate wao Zebedeo m'chombomo pamodzi ndi antchito olembedwa, namtsata.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo pomwepo anawaitana: ndipo anasiya atate wao Zebedeo m'chombomo pamodzi ndi antchito olembedwa, namtsata.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 nthaŵi yomweyo Iye nkuŵaitana. Pamenepo iwowo adasiya bambo wao Zebedeo m'chombomo pamodzi ndi antchito ake, namatsata Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Mosataya nthawi anawayitana, ndipo anasiya abambo awo Zebedayo ndi anyamata aganyu ali mʼbwatomo, namutsata Iye.

Onani mutuwo Koperani




Marko 1:20
11 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anasiya ng'ombe zija, namthamangira Eliya, nati, Ndiloleni ndiyambe ndakampsompsona atate wanga ndi amai wanga; nditatero ndidzakutsatani. Nati iye, Bwerera ndakuchitanji?


Iye wakukonda atate wake, kapena amake koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wakukonda mwana wake wamwamuna, kapena wamkazi koposa Ine, sayenera Ine.


Ndipo atapita patsogolo pang'ono, anaona Yakobo, mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake, iwonso anali m'chombo nakonza makoka ao.


Ndipo iwo analowa mu Kapernao; ndipo pomwepo pa tsiku la Sabata iye analowa m'sunagoge naphunzitsa.


Yesu anati, Ndithu ndinena ndi inu, Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amai, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwinowo,


Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sangathe kukhala wophunzira wanga.


Ndipo m'mene iwo anakocheza ngalawa zao pamtunda, anasiya zonse, namtsata Iye.


Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.


amene anati za atate wake ndi amai wake, sindinamuone; Sanazindikire abale ake, sanadziwe ana ake omwe; popeza anasamalira mau anu, nasunga chipangano chanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa