Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 1:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo pakuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andrea, mbale wake wa Simoni, alinkuponya khoka m'nyanja; pakuti anali asodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo pakuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andrea, mbale wake wa Simoni, alinkuponya khoka m'nyanja; pakuti anali asodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Pamene Yesu ankayenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, adaona anthu aŵiri, Simoni ndi mbale wake Andrea, akuponya khoka m'nyanjamo, popeza kuti anali asodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja, popeza anali asodzi.

Onani mutuwo Koperani




Marko 1:16
11 Mawu Ofanana  

Ndipo maina ao a atumwiwo khumi ndi awiri ndi awa: woyamba Simoni wotchedwa Petro, ndi Andrea mbale wake; Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake;


Ndipo Simoni anamutcha Petro;


ndi Andrea, ndi Filipo, ndi Bartolomeo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo, ndi Simoni Mkanani,


Simoni, amene anamutchanso Petro, ndi Andrea mbale wake, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Filipo, ndi Bartolomeo,


Filipo anadza nanena kwa Andrea; nadza Andrea ndi Filipo, nanena ndi Yesu.


Mmodzi wa ophunzira ake, Andrea, mbale wake wa Simoni Petro, ananena ndi Iye,


Ndipo pamene adalowa, anakwera kuchipinda chapamwamba, kumene analikukhalako; ndiwo Petro ndi Yohane ndi Yakobo ndi Andrea, Filipo ndi Tomasi, Bartolomeo ndi Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni Zelote, ndi Yudasi mwana wa Yakobo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa