Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Maliro 5:2 - Buku Lopatulika

2 Cholowa chathu chasanduka cha alendo, ndi nyumba zathu za achilendo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Cholowa chathu chasanduka cha alendo, ndi nyumba zathu za achilendo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Choloŵa chathu chaperekedwa kwa alendo, nyumba zathu zili m'manja mwa anthu akudza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Apereka cholowa chathu kwa obwera, nyumba zathu kwa alendo.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 5:2
13 Mawu Ofanana  

Wokongoletsa agwire zonse ali nazo; ndi alendo alande za ntchito yake.


Dziko lanu lili bwinja; mizinda yanu yatenthedwa ndi moto; dziko lanu alendo alimkudya pamaso panu; ndipo lili labwinja monga lagubuduzidwa ndi alendo.


Pamenepo anaankhosa adzadyapo ngati m'busa mwao, ndi malo a bwinja a zonenepa zachilendo zidzadyapo.


Anthu anu opatulika anakhala nacho kanthawi kokha; adani athu apondereza Kachisi wanu wopatulika.


Iwe, iwe wekha, udzaleka pa cholowa chako chimene ndinakupatsa iwe; ndipo ndidzakutumikiritsa adani ako m'dziko limene sulidziwa; pakuti wakoleza moto m'mkwiyo wanga umene udzatentha kunthawi zamuyaya.


Nyumba zao zidzasanduka za ena, pamodzi ndi minda yao ndi akazi ao; pakuti ndidzatambasula dzanja langa pa okhala m'dziko, ati Yehova.


Ndipo ndidzachipereka m'dzanja la alendo chikhale cholandika, ndi kwa oipa a m'dziko chikhale chofunkha; ndipo adzachiipsa.


Chifukwa chake ndidzabwera nao amitundu oipitsitsa, ndipo iwo adzalandira nyumba zao ngati cholowa, ndidzaleketsanso kudzikuza kwa amphamvu, kuti adetsedwe malo ao opatulika.


Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kamvulumvulu; alibe tirigu wosasenga; ngala siidzatulutsa ufa; chinkana iutulutsa, alendo adzaumeza.


Israele wamezedwa; tsopano ali mwa amitundu ngati chotengera choti munthu sakondwera nacho.


Ndipo zolemera zao zidzakhala zakufunkhidwa; ndi nyumba zao zabwinja; adzamangadi nyumba, koma sadzagonamo; adzaoka minda yampesa koma sadzamwa vinyo wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa