Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Maliro 4:9 - Buku Lopatulika

9 Ophedwa ndi lupanga amva bwino kupambana ophedwa ndi njala; pakuti amenewa angokwalika napyozedwa, posowa zipatso za m'munda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ophedwa ndi lupanga amva bwino kupambana ophedwa ndi njala; pakuti amenewa angokwalika napyozedwa, posowa zipatso za m'munda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Amene adaphedwa pa nkhondo anali amwai kwambiri kupambana amene adafa ndi njala. Ameneŵa ankafooka pang'onopang'ono mpaka kutsirizika, chifukwa chosoŵa chakudya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Amene anaphedwa ndi lupanga aliko bwino kuposa amene anafa ndi njala; chifukwa chosowa chakudya cha mʼmunda iwowa ankafowoka ndi njala mpaka kufa.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 4:9
10 Mawu Ofanana  

Tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi wachinai njala idakula m'mzindamo, panalibe chakudya kwa anthu a m'dzikomo.


nanena nao ana a Israele, Ha? Mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m'dziko la Ejipito, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife chokhuta; pakuti mwatitulutsa kudza nafe m'chipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala.


Iwe amene wadzala ndi zimfuu, mzinda waphokoso, mzinda wokondwa; ophedwa ako sanaphedwe ndi lupanga, sanafe m'nkhondo.


Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za kumlengalenga, ndi zilombo za dziko lapansi.


Ndi zilemba zanu zidzakhala pamitu panu, ndi nsapato zanu kumapazi anu, simudzachita chisoni kapena kulira, koma mudzaonda ndi mphulupulu zanu, ndi kubulirana wina ndi mnzake.


Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, nena kwa nyumba ya Israele, Mumatero inu ndi kuti, Zolakwa zathu ndi zochimwa zathu zitikhalira, ndipo tichita nazo liwondewonde, tidzakhala ndi moyo bwanji?


Nanenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndidzathyola mchirikizo, ndiwo chakudya, mu Yerusalemu; ndipo adzadya chakudyacho monga mwa muyeso, ndi mosamalira, nadzamwa madzi monga mwa muyeso, ndi kudabwa;


Kunja kuli lupanga, ndi m'katimo muli mliri ndi njala; wokhala kuthengo adzafa ndi lupanga, ndi wokhala m'mzindawo njala ndi mliri zidzamutha.


Ndipo otsala mwa inu adzazunzika m'moyo ndi mphulupulu zao m'maiko a adani anu; ndiponso ndi mphulupulu za makolo ao adzazunzika m'moyo.


ndipo adzadya zipatso za ng'ombe zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, kufikira mwaonongeka; osakusiyirani tirigu, vinyo, kapena mafuta, zoswana ng'ombe zanu, zoswana nkhosa zanu, kufikira atakuonongani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa