Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 4:10 - Buku Lopatulika

10 Manja a akazi achisoni anaphika ana aoao; anali chakudya chao poonongeka mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Manja a akazi achisoni anaphika ana aoao; anali chakudya chao poonongeka mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ngakhale akazi achifundo ndi manja ao omwe adafika pophika ana ao. Ana aowo adasanduka chakudya chao pa nthaŵi imene anthu anga adaonongedwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Amayi achifundo afika pophika ana awo enieni, ndiwo anali chakudya chawo pamene anthu anga anali kuwonongeka.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 4:10
12 Mawu Ofanana  

Tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi wachinai njala idakula m'mzindamo, panalibe chakudya kwa anthu a m'dzikomo.


Iwe amene wadzala ndi zimfuu, mzinda waphokoso, mzinda wokondwa; ophedwa ako sanaphedwe ndi lupanga, sanafe m'nkhondo.


Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wombala iye? Inde awa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.


Ndipo ndidzadyetsa iwo mnofu wa ana ao aamuna ndi aakazi, ndipo adzadya yense mnofu wa mbale wake, m'nkhondo yozinga ndi m'kupsinjikako, kumene adani ao, ndi iwo akufuna moyo wao, adzapsinja iwo nako.


Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka; chiwindi changa chagwa pansi chifukwa cha kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga; chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mzindawu.


Onani Yehova, nimupenye, mwachitira ayani ichi? Kodi akazi adzadya zipatso zao, kunena ana amene anawalera wokha? Kodi wansembe ndi mneneri adzaphedwa m'malo opatulika a Ambuye?


M'diso mwanga mutsika mitsinje ya madzi chifukwa cha mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga woonongedwa.


Angakhale ankhandwe amapatsa bere, nayamwitsa ana ao; koma mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga wasanduka wankhanza, ngati nthiwatiwa za m'chipululu.


Chifukwa chake atate adzadya ana pakati pako, ndi ana adzadya atate ao; ndipo ndidzachita maweruzo mwa iwe, ndi akutsala onse ndidzawabalalitsa kumphepo zonse.


Ndipo mudzadya nyama ya ana anu aamuna; inde nyama ya ana anu aakazi mudzaidya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa