Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Maliro 4:4 - Buku Lopatulika

4 Lilime la mwana woyamwa limamatira kumalakalaka kwake ndi ludzu; ana aang'ono apempha mkate koma palibe wakuwanyemera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Lilime la mwana woyamwa limamatira kumalakalaka kwake ndi ludzu; ana ang'ono apempha mkate koma palibe wakuwanyemera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Lilime la mwana wakhanda limakangamira kukhosi chifukwa cha ludzu. Ana aang'ono amafuna chakudya, koma palibe woŵapatsa mpang'ono pomwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Lilime la mwana lakangamira kukhosi chifukwa cha ludzu, ana akupempha chakudya, koma palibe amene akuwapatsa.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 4:4
12 Mawu Ofanana  

Koma kazembeyo ananena nao, Ngati mbuyanga ananditumiza kwa mbuyako, ndi kwa iwe, kunena mau awa? Si kwa anthu awa nanga okhala palinga, kuti akadye zonyansa zao, ndi kumwa mkodzo wao pamodzi ndi inu?


Tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi wachinai njala idakula m'mzindamo, panalibe chakudya kwa anthu a m'dzikomo.


Lilime langa limamatike kunsaya zanga, ndikapanda kukumbukira inu; ndikapanda kusankha Yerusalemu koposa chimwemwe changa chopambana.


Mphamvu yanga yauma ngati phale; ndi lilime langa likangamira kunsaya zanga; ndipo mwandifikitsa kufumbi la imfa.


Chifukwa chake anthu anga amuka m'nsinga, chifukwa cha kusowa nzeru; ndi amuna ao olemekezeka ali ndi njala, ndi khamu lao lauma kukhosi.


Akulu ao atuma ang'ono ao kumadzi; afika kumaenje, osapeza madzi; abwera ndi mitsuko yao yopanda kanthu; ali ndi manyazi, athedwa nzeru, afunda mitu yao.


Anthu ake onse ausa moyo nafunafuna mkate; ndi zokondweretsa zao agula zakudya kuti atsitsimutse moyo wao; taonani, Yehova, nimupenye; pakuti ndasanduka wonyansa.


Lingakhale fumbi lochokera kumudzi kwanu, lomamatika kumapazi athu, tilisansira pa inu; koma zindikirani ichi, kuti Ufumu wa Mulungu wayandikira.


chifukwa chake mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lachitsulo pakhosi panu, kufikira atakuonongani.


Adzaonda nayo njala adzanyekeka ndi makala a moto, chionongeko chowawa; ndipo ndidzawatumizira mano a zilombo, ndi ululu wa zokwawa m'fumbi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa