Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Maliro 4:3 - Buku Lopatulika

3 Angakhale ankhandwe amapatsa bere, nayamwitsa ana ao; koma mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga wasanduka wankhanza, ngati nthiwatiwa za m'chipululu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Angakhale ankhandwe amapatsa bere, nayamwitsa ana ao; koma mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga wasanduka wankhanza, ngati nthiwatiwa za m'chipululu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ngakhale nkhandwe siziwumira bere, zimayamwitsa ana. Koma anthu anga ndi ankhalwe, ali ngati nthiŵatiŵa zakunkhalango.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ngakhale nkhandwe zimapereka bere kuyamwitsa ana ake, koma anthu anga asanduka ankhanza ngati nthiwatiwa mʼchipululu.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 4:3
14 Mawu Ofanana  

Ndipo pouka ine m'mawa kuyamwitsa mwana wanga ndaona, ngwakufa, koma nditamzindikira m'mawa ndaona si mwana wanga wobala ine ai.


Ndipo mimbulu idzalira m'maboma ao, ndi ankhandwe m'manyumba ao abwino; ndi nthawi yake iyandikira, ndi masiku ake sadzachuluka.


Ndipo minga idzamera m'nyumba zake zazikulu, khwisa ndi mitungwi m'malinga mwake; ndipo adzakhala malo a ankhandwe, ndi bwalo la nthiwatiwa.


Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wombala iye? Inde awa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.


Ndipo ndidzadyetsa iwo mnofu wa ana ao aamuna ndi aakazi, ndipo adzadya yense mnofu wa mbale wake, m'nkhondo yozinga ndi m'kupsinjikako, kumene adani ao, ndi iwo akufuna moyo wao, adzapsinja iwo nako.


Onani Yehova, nimupenye, mwachitira ayani ichi? Kodi akazi adzadya zipatso zao, kunena ana amene anawalera wokha? Kodi wansembe ndi mneneri adzaphedwa m'malo opatulika a Ambuye?


Manja a akazi achisoni anaphika ana aoao; anali chakudya chao poonongeka mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga.


Chifukwa chake atate adzadya ana pakati pako, ndi ana adzadya atate ao; ndipo ndidzachita maweruzo mwa iwe, ndi akutsala onse ndidzawabalalitsa kumphepo zonse.


Ndipo mudzadya nyama ya ana anu aamuna; inde nyama ya ana anu aakazi mudzaidya.


opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda chikondi cha chibadwidwe, opanda chifundo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa