Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Maliro 4:2 - Buku Lopatulika

2 Ana a Ziyoni a mtengo wapatali, olingana ndi golide woyengetsa, angoyesedwa ngati mbiya zadothi zozipanga manja a woumba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ana a Ziyoni a mtengo wapatali, olingana ndi golide woyengetsa, angoyesedwa ngati mbiya zadothi zozipanga manja a woumba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Onani ana okondedwa a m'Ziyoni amene kale anali ngati golide kwa ife, tsopano akuŵayesa mbiya zadothi zimene woumba amachita kuumba ndi manja ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Haa! Ana a Ziyoni amtengowapatali amene kale anali ngati golide, tsopano ali ngati miphika ya dothi, ntchito ya owumba mbiya!

Onani mutuwo Koperani




Maliro 4:2
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Iye adzagumulapo, monga mbiya ya woumba isweka, ndi kuiswaiswa osaileka; ndipo sipadzapezedwa m'zigamphu zake phale lopalira moto pachoso, ngakhale lotungira madzi padziwe.


Palibenso wina wakumtsogolera mwa ana aamuna onse, amene iye anawabala; palibe wina amgwira dzanja mwa ana onse anawalera.


Atero Yehova, Pita, nugule nsupa ya woumba, nutenge akulu a anthu, ndi akulu a ansembe;


nuziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Chomwecho ndidzaphwanya anthu awa ndi mzinda uwu, monga aphwanya mbiya ya woumba, imene sangathe kuiumbanso, ndipo adzaika maliro mu Tofeti, mpaka mulibe malo akuikamo.


Kodi munthu uyu Koniya ndiye mbiya yopepuka yosweka? Kodi ndiye mbiya yosakondweretsa? Chifukwa chanji atulutsidwa iye, ndi mbeu zake, ndi kuponyedwa m'dziko limene salidziwa?


Wamng'ono ndi nkhalamba agona pansi m'makwalala; anamwali ndi anyamata anga agwa ndi lupanga; munawapha tsiku la mkwiyo wanu, munawagwaza osachitira chisoni.


Anawapachika akalonga manja ao; sanalemekeze nkhope za akulu.


Israele wamezedwa; tsopano ali mwa amitundu ngati chotengera choti munthu sakondwera nacho.


Pakuti ndadzikokera Yuda, ndadzaza uta ndi Efuremu; ndipo ndidzautsa ana ako, Ziyoni, alimbane nao ana ako, Yavani, ndipo ndidzakuyesa lupanga la ngwazi.


Koma tili nacho chuma ichi m'zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife;


Koma m'nyumba yaikulu simuli zotengera za golide ndi siliva zokha, komatunso za mtengo ndi dothi; ndipo zina zaulemu, koma zina zopanda ulemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa