Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Maliro 2:9 - Buku Lopatulika

9 Zipata zake zalowa pansi; waononga ndi kuthyola mipiringidzo yake; mfumu yake ndi akalonga ake ali pakati pa amitundu akusowa chilamulo; inde, aneneri ake samalandira masomphenya kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Zipata zake zalowa pansi; waononga ndi kuthyola mipiringidzo yake; mfumu yake ndi akalonga ake ali pakati pa amitundu akusowa chilamulo; inde, aneneri ake samalandira masomphenya kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Zipata za mzindawo zakwiririka pansi. Mipiringidzo yake yathyoka ndi kusakazika. Mfumu yake ndi akalonga ake ali ku ukapolo pakati pa anthu akunja, malamulo a Mulungu palibenso oŵalalika. Aneneri ake omwe sakuchitanso zija zoona zinthu m'masomphenya zochokera kwa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Zipata za Yerusalemu zalowa pansi; wathyola ndi kuwononga mipiringidzo yake. Mfumu ndi akalonga ake agwidwa ukapolo pakati pa mitundu ya anthu, palibenso lamulo, ndipo aneneri ake sakupeza masomphenya kuchokera kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 2:9
27 Mawu Ofanana  

Napha ana a Zedekiya pamaso pake, namkolowola Zedekiya maso ake, nammanga ndi maunyolo amkuwa, namuka naye ku Babiloni.


Masiku ambiri tsono Israele anakhala wopanda Mulungu woonayo, ndi wopanda wansembe wakuphunzitsa, ndi wopanda chilamulo;


Nanena nane iwo, Otsalawo otsala andende uko kudzikoko akulukutika kwakukulu, nanyozedwa; ndi linga la Yerusalemu lapasuka, ndi zipata zake zatenthedwa ndi moto.


Sitiziona zizindikiro zathu; palibenso mneneri; ndipo mwa ife palibe wina wakudziwa mpaka liti.


M'mzinda mwatsala bwinja, ndi chipata chamenyedwa ndi chipasuko.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Aneneri anenera zonama m'dzina langa; sindinatume iwo, sindinauze iwo, sindinanene nao; anenera kwa inu masomphenya onama, ndi ula, ndi chinthu chachabe, ndi chinyengo cha mtima wao.


Yehova wa makamu atero, Musamvere mau a aneneri amene anenera kwa inu; akuphunzitsani zachabe; anena masomphenya a mtima wao, si a m'kamwa mwa Yehova.


Chaka chakhumi ndi chimodzi cha Zedekiya, mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai, mzinda unabooledwa.


Ndipo Ababiloni anatentha ndi moto nyumba ya mfumu, ndi nyumba za anthu, nagumula malinga a Yerusalemu.


Olimba a ku Babiloni akana kumenyana, akhala m'malinga ao; mphamvu yao yalephera; akhala ngati akazi; nyumba zake zapsa ndi moto; akapichi ake athyoka.


Ndipo nkhondo yonse ya Ababiloni, imene inali ndi kapitao wa alonda, inagumula makoma onse a Yerusalemu pomzungulira pake.


Yuda watengedwa ndende chifukwa cha msauko ndi ukapolo waukulu; akhala mwa amitundu, sapeza popuma; onse akumlondola anampeza pakati popsinjikiza.


Amafuula kwa iwo, Chokani, osakonzeka inu, chokani, chokani, musakhudze kanthu. Pothawa iwo ndi kusochera, anthu anati kwa amitundu, Sadzagoneranso kuno.


Wodzozedwa wa Yehova, ndiye mpweya wa m'mphuno mwathu, anagwidwa m'maenje ao; amene tinanena kuti, Tidzakhala m'mthunzi mwake pakati pa amitundu,


Ndidzamphimba ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzafika naye ku Babiloni, ku dziko la Ababiloni; sadzaliona, chinkana adzafako.


Ndidzamphimbanso ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzadza naye ku Babiloni, ndi kunena naye komweko mlandu wa kulakwa kwake anandilakwira nako.


Lidzafika tsoka lotsatanatsatana, kudzakhalanso mbiri yotsatanatsatana, ndipo adzafunafuna masomphenya a mneneri, koma malamulo adzatayikira wansembe, uphungu ndi kutayikira akulu.


Ndi lupanga lidzagwera mizinda yake, lidzatha mipiringidzo yake, ndi kuononga chifukwa cha uphungu wao.


Pakuti ana a Israele adzakhala masiku ambiri opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda choimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi;


Ndipo ndidzathyola mpiringidzo wa Damasiko, ndi kulikha okhala m'chigwa cha Aveni, ndi iye wogwira ndodo yachifumu mu Betedeni; ndi anthu a Aramu adzalowa ndende ku Kiri, ati Yehova.


Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simuudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu ina ya mitengo ndi miyala.


Ndipo kudzali kuti, monga Yehova anakondwera nanu kukuchitirani zabwino, ndi kukuchulukitsani; momwemo Yehova adzakondwera nanu kutayikitsa ndi kuononga inu, ndipo adzakuzulani kudziko kumene mulowako kulilandira.


Ndipo pamene Saulo anafunsira kwa Yehova, Yehova sanamyankhe ngakhale ndi maloto, kapena ndi Urimu, kapena ndi aneneri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa