Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 2:10 - Buku Lopatulika

10 Akulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi natonthola; aponya fumbi pa mitu yao, anamangirira chiguduli m'chuuno mwao: Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa pansi mitu yao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Akulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi natonthola; aponya fumbi pa mitu yao, anamangirira chiguduli m'chuuno mwao: Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa pansi mitu yao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Akuluakulu a mu mzinda wa Ziyoni, akhala pansi atangoti chete. Adzithira fumbi kumutu, ndipo avala ziguduli. Anamwali a ku Yerusalemu aŵeramitsa mitu yao pansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Akuluakulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala chete pansi; awaza fumbi pa mitu yawo ndipo avala ziguduli. Anamwali a Yerusalemu aweramitsa mitu yawo pansi.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 2:10
26 Mawu Ofanana  

Ndipo Tamara anathira phulusa pamutu pake, nang'amba chovala cha mawangamawanga chimene analikuvala, nagwira dzanja lake pamutu pake, namuka nayenda, nalira komveka.


M'makwalala mwao adzimangira chiguduli m'chuuno, pamwamba pa nyumba zao, ndi m'malo a mabwalo ao, yense akuwa, naliritsa kwambiri.


Ndipo padzakhala m'malo mwa zonunkhiritsa mudzakhala zovunda; ndi m'malo mwa lamba chingwe; ndipo m'malo mwa tsitsi labwino dazi; m'malo mwa chovala chapachifuwa mpango wachiguduli; zipsera m'malo mwa ukoma.


Ndipo zipata zake zidzalira maliro; ndipo iye adzakhala bwinja, nadzakhala pansi.


Ndipo anafika Eliyakimu, mwana wa Hilikiya, amene anali wapa nyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi Yowa, mwana wa Asafu, mkumbutsi, kwa Hezekiya ndi zovala zao zong'ambika, namuuza iye mau a kazembeyo.


Tsika, ukhale m'fumbi, namwaliwe, mwana wamkazi wa Babiloni; khala pansi popanda mpando wachifumu, mwana wamkazi wa Ababiloni, pakuti iwe sudzayesedwanso wozizira ndi wololopoka.


Khala iwe chete, lowa mumdima, mwana wamkazi wa Ababiloni; pakuti sudzatchedwanso mkazi wa maufumu.


Tikhaliranji ife? Tasonkhanani, tilowe m'mizinda yamalinga, tikhale chete m'menemo; pakuti Yehova Mulungu wathu watikhalitsa ife chete, natipatsa ife madzi a ndulu timwe, pakuti tamchimwira Yehova.


Ha! Mzindawo unadzala anthu, ukhalatu pa wokha! Ukunga mkazi wamasiye! Waukuluwo mwa amitundu, kalonga wamkazi m'madera a dziko wasanduka wolamba!


M'njira za Ziyoni mulira posoweka akudzera msonkhano; pa zipata zake zonse papasuka; ansembe ake onse ausa moyo; anamwali ake asautsidwa; iye mwini namva zowawa.


Akhale pa yekha, natonthole, pakuti Mulungu wamsenzetsa ilo.


Mkwiyo wa Yehova unawalekanitsa, sadzawasamaliranso; iwo sanalemekeze ansembe, sanakomere mtima akulu.


Omwe anadya zolongosoka angosiyidwa m'makwalala; omwe analeredwa navekedwa mlangali afungatira madzala.


Anawapachika akalonga manja ao; sanalemekeze nkhope za akulu.


Akulu adatha kuzipata, anyamata naleka nyimbo zao.


nadzamveketsa mau ao pa iwe, nadzalira mowawa mtima, nadzathira fumbi pamitu pao, nadzakunkhulira m'maphulusa,


nadzameta mpala chifukwa cha iwe, nadzadzimangira ziguduli m'chuuno, nadzakulirira ndi mtima wowawa maliro owawa.


Ndipo adzadzimangira m'chuuno ndi ziguduli, ndi zoopsetsa zidzawaphimba, ndi nkhope zonse zidzachita manyazi, ndi mitu yao yonse idzachita dazi.


Lirani ngati namwali wodzimangira m'chuuno chiguduli, chifukwa cha mwamuna wa unamwali wake.


Chifukwa chake wochenjerayo akhala chete nthawi yomweyo; pakuti ndiyo nthawi yoipa.


Tsiku lomwelo anamwali okongola ndi anyamata adzakomoka nalo ludzu.


Koma nyimbo za ku Kachisi zidzasanduka kubuma tsiku ilo, ati Ambuye Yehova; mitembo idzachuluka; adzaitaya paliponse padzakhala zii.


Pakuti mau awa anafikira mfumu ya Ninive, ndipo inanyamuka kumpando wake wachifumu, nivula chofunda chake, nifunda chiguduli, nikhala m'maphulusa.


Ndipo Yoswa anang'amba zovala zake, nagwa nkhope yake pansi, ku likasa la Yehova, mpaka madzulo, iye ndi akuluakulu a Israele, nathira fumbi pamitu pao.


Ndipo anathira fumbi pamitu pao, nafuula, ndi kulira, ndi kuchita maliro, nanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukuluwo, umene analemerezedwa nao onse akukhala nazo zombo panyanja, chifukwa cha kulemera kwake, pakuti mu ora limodzi unasanduka bwinja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa