Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 2:8 - Buku Lopatulika

8 Yehova watsimikiza mtima kupasula linga la mwana wamkazi wa Ziyoni; watambalika chingwe, osabweza dzanja lake kuti lisaonongepo; waliritsa tchemba ndi linga; zilefuka pamodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Yehova watsimikiza mtima kupasula linga la mwana wamkazi wa Ziyoni; watambalika chingwe, osabweza dzanja lake kuti lisaonongepo; waliritsa tchemba ndi linga; zilefuka pamodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Chauta adaatsimikiza zoti aononge malinga a mzinda wa Ziyoni. Adauyesa ndi chingwe chake, ndipo sadafune kuleka kuuwononga kotheratu. Adaliritsa okhala pa malinga ndi pa makoma ake, onsewo akuzunzikira limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Yehova anatsimikiza kugwetsa makoma a mwana wamkazi wa Ziyoni. Anawayesa ndi chingwe ndipo sanafune kuleka kuwagwetsa. Analiritsa malinga ndi makoma; onse anawonongeka pamodzi.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 2:8
17 Mawu Ofanana  

Ndipo anakantha Amowabu nawayesa ndi chingwe, nawagonetsa pansi; ndipo anawayesera zingwe ziwiri kupha, ndi chingwe chimodzi chathunthu kusunga ndi moyo. Ndipo Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nayo mitulo.


Ndipo ndidzayesa pa Yerusalemu chingwe choongolera cha Samariya, ndi chingwe cholungamitsira chilili cha nyumba ya Ahabu; ndidzapukuta Yerusalemu monga umo apukutira mbale, kuipukuta ndi kuivundikira.


Mundichotsere dzanja lanu kutali, ndi kuopsa kwanu kusandichititse mantha.


Pakuti nditsiku laphokoso, ndi lopondereza pansi, ndi lothetsa nzeru, lochokera kwa Ambuye, Yehova wa makamu, m'chigwa cha masomphenya, kugumuka kwa malinga, ndi kufuulira kumapiri.


Ndipo ndidzayesa chiweruziro chingwe choongolera, ndi chilungamo chingwe cholungamitsira chilili; ndipo matalala adzachotsa pothawirapo mabodza, ndi madzi adzasefukira mobisalamo.


Ndipo zipata zake zidzalira maliro; ndipo iye adzakhala bwinja, nadzakhala pansi.


Koma vuwo ndi nungu zidzakhalamo, ndipo kadzidzi ndi khwangwala adzakhala m'menemo, ndipo Mulungu adzatambalika pamenepo chingwe choongolera cha chisokonezo, ndi chingwe cholungamitsa chilili chosatha kuchita kanthu.


Ndipo tsopano ndidzakuuzani chimene nditi ndichite ndi munda wanga wampesa; ndidzachotsapo tchinga lake, ndipo zidzadyedwa; ndidzagumula linga lake ndipo zidzapondedwa pansi;


Yuda alira, ndipo zipata zake zilefuka, zikhala pansi zovekedwa ndi zakuda; mfuu wa Yerusalemu wakwera.


Kwerani pa makoma ake nimupasule; koma musatsirize konse; chotsani nthambi zake pakuti sizili za Yehova.


ndipo anatentha nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu, ngakhale zinyumba zazikulu zonse, anazitentha ndi moto.


Yehova wachita chomwe analingalira; watsiriza mau ake, amene analamulira nthawi yakale; wagwetsa osachitira chisoni; wakondweretsa adani pa iwe, wakweza nyanga ya amaliwongo ako.


Mtima wao unafuula kwa Ambuye, linga iwe la mwana wamkazi wa Ziyoni, igwe misozi ngati mtsinje usana ndi usiku; usapume kanthawi, asaleke mwana wa diso lako.


Ambuye wameza nyumba zonse za Yakobo osazichitira chisoni; wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wake; wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ake.


Ambuye wasanduka mdani, wameza Israele; wameza zinyumba zake zonse, wapasula malinga ake; nachulukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi chibumo.


Koma ndinabweza dzanja langa ndi kuchichita, chifukwa cha dzina langa; kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu, amene ndinawatulutsa pamaso pao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa