Maliro 2:2 - Buku Lopatulika2 Ambuye wameza nyumba zonse za Yakobo osazichitira chisoni; wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wake; wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Yehova wameza nyumba zonse za Yakobo osazichitira chisoni; wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wake; wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Chauta adaononga midzi yonse ya Yakobe popanda ndi chifundo chomwe. Chifukwa cha kupsa mtima adathyola malinga a mizinda ya Yuda. Adagwetsera pansi mochititsa manyazi, ufumu wa Israele ndi olamulira ake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Ambuye anawononga midzi yonse ya Yakobo mopanda chifundo; mu mkwiyo wake anagwetsa malinga a mwana wamkazi wa Yuda. Anagwetsa pansi mochititsa manyazi maufumu ndi akalonga ake. Onani mutuwo |
Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m'mzinda uwu amene asiyidwa ndi mliri, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo.