Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Malaki 1:12 - Buku Lopatulika

12 Koma inu muliipsa, pakunena inu, Gome la Ambuye laipsidwa, ndi zipatso zake, chakudya chake, chonyozeka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Koma inu muliipsa, pakunena inu, Gome la Yehova laipsidwa, ndi zipatso zake, chakudya chake, chonyozeka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 “Koma inuyo mumalinyoza ponena kuti tebulo la Chauta nlachabechabe, ndipo chakudya chopereka pamenepo nchonyozeka.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 “Koma inu mumalinyoza ponena kuti tebulo la Ambuye, ‘ndi lodetsedwa,’ ndipo chakudya chake, ‘nʼchonyozeka!’

Onani mutuwo Koperani




Malaki 1:12
13 Mawu Ofanana  

Koma popeza pakuchita ichi munapatsa chifukwa chachikulu kwa adani a Yehova cha kuchitira mwano, mwanayonso wobadwira inu adzafa ndithu.


Guwa la nsembe linali lamtengo, msinkhu wake mikono itatu, ndi m'litali mwake mikono iwiri, ndi ngodya zake, ndi tsinde lake, ndi thupi, nza mtengo; ndipo ananena ndi ine, Ili ndiko gome lili pamaso pa Yehova.


iwowa adzalowa m'malo anga opatulika, nadzayandikira kugome langa kunditumikira, nadzasunga udikiro wanga.


Israele, chikuononga ndi ichi, chakuti utsutsana ndi Ine, chithandizo chako.


Ndipo usamapereka a mbumba yako kuwapitiriza kumoto chifukwa cha Moleki; usamaipsa dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.


ndiwo amene aliralira fumbi lapansi lili pamutu pa wosauka, napotoza njira ya wofatsa; ndipo munthu ndi atate wake amuka kwa namwali yemweyo, kuti aipse dzina langa loyera;


Mukutinso, Taonani, ncholemetsa ichi! Ndipo mwachipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira kudzanja lanu? Ati Yehova.


Koma inu mwapatuka m'njira; mwakhumudwitsa ambiri m'chilamulo; mwaipsa chipangano cha Levi, ati Yehova wa makamu.


Pakuti dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu a mitundu, monga mwalembedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa