Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 9:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ake, sanapenye kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye mu Damasiko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ake, sanapenya kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye m'Damasiko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Saulo adadzuka, koma pamene maso ake adaphenyuka, sadathe kupenya kanthu. Tsono anzake aja adamgwira pa dzanja naloŵa naye m'Damasiko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Saulo anayimirira, ndipo pamene anatsekula maso ake sanathe kuona. Kotero anamugwira dzanja ndi kulowa naye mu Damasiko.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 9:8
10 Mawu Ofanana  

Ndipo anadzigawanizira iwo usiku, iye ndi anyamata ake, nawakantha, nawapirikitsa kufikira ku Hoba, ndiko ku dzanja lamanzere la ku Damasiko.


Ndipo anachititsa khungu m'maso mwa anthu amene anali pakhomo pa nyumba, aang'ono ndi aakulu, ndipo anavutika kufufuza pakhomo.


Koma Yehova ananena naye, Anampangira munthu m'kamwa ndani? Kapena analenga munthu wosalankhula ndani, kapena wogontha, kapena wamaso, kapena wakhungu? Si ndine Yehova kodi?


Ndipo tsopano, taona, dzanja la Ambuye lili pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu wosapenya dzuwa nthawi. Ndipo pomwepo lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo anamukamuka nafuna wina womgwira dzanja.


Ndipo popeza sindinapenye, chifukwa cha ulemerero wa kuunikako, anandigwira dzanja iwo amene anali ndi ine, ndipo ndinafika ku Damasiko.


Ndipo pomwepo padagwa kuchoka m'maso mwake ngati mamba, ndipo anapenyanso; ndipo ananyamuka nabatizidwa;


Ndipo anakhala masiku atatu wosaona, ndipo sanadye kapena kumwa.


Mu Damasiko kazembe wa mfumu Areta analindizitsa mzinda wa Adamasiko kuti andigwire ine;


kapena kukwera kunka ku Yerusalemu sindinankako kwa iwo amene anakhala atumwi ndisanakhale mtumwi ine, komatu ndinamuka ku Arabiya, ndipo ndinabweranso ku Damasiko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa