Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 9:41 - Buku Lopatulika

41 Ndipo Petro anamgwira dzanja, namnyamutsa; ndipo m'mene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Ndipo Petro anamgwira dzanja, namnyamutsa; ndipo m'mene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Petro adamgwira dzanja namuimiritsa. Ndipo adaitana anthu a Mulungu ndi azimai amasiye aja, nampereka kwa iwo ali wamoyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Petro anamugwira dzanja, namuyimiritsa. Ndipo anayitana okhulupirira ndi amasiye namupereka wamoyo.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 9:41
15 Mawu Ofanana  

Ndipo anamfotokozera iye kuti, Yosefe akali ndi moyo, ndipo alamulira m'dziko lonse la Ejipito. Pamenepo mtima wake unakomoka, pakuti sanawakhulupirire iwo.


Ndipo Eliya ananyamula mwanayo, natsika naye ku chipinda chosanja, nalowa naye m'nyumba, nampereka kwa amake; nati, Eliya, Taona, mwana wako ali moyo.


Nati, Katole. Natambasula dzanja lake, naitenga.


Dalitso la iye akati atayike linandidzera, ndi mtima wa mkazi wamasiye ndinauimbitsa mokondwera.


Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.


ndipo anadza namgwira dzanja, namuutsa; ndipo malungo anamleka, ndipo anawatumikira iwo.


Ndipo pamene anayandikira kuchipata cha mzindawo, onani, anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri amumzinda anali pamodzi naye.


Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amake.


Ndipo anadza naye mnyamata ali wamoyo, natonthozedwa kwakukulu.


Ndipo anamgwira iye kudzanja lake lamanja, namnyamutsa; ndipo pomwepo mapazi ake ndi mfundo za kumapazi zinalimbikitsidwa.


Koma masiku awo, pakuchulukitsa ophunzira, kunauka chidandaulo, Agriki kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye ao anaiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku.


Ndipo Ananiya anayankha nati, Ambuye, ndamva ndi ambiri za munthu uyu, kuti anachitiradi choipa oyera mtima anu mu Yerusalemu;


Koma kunali, pakupita Petro ponseponse, anatsikiranso kwa oyera mtima akukhala ku Lida.


Chitira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu.


Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m'mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa