Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 9:40 - Buku Lopatulika

40 Koma Petro anawatulutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ake; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

40 Koma Petro anawatulutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ake; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

40 Petro adaŵapempha onse kuti atuluke, ndipo adagwada pansi nkumapemphera. Kenaka adatembenukira mtembo uja nati, “Tabita, dzuka!” Apo Tabita adatsekula maso, ndipo pamene adaona Petro, adakhala tsonga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

40 Petro anatulutsa anthu onse mʼchipindamo; ndipo anagwada pansi ndi kupemphera. Anatembenukira mtembo uja nati, “Tabita, dzuka,” Tabita anatsekula maso ake, ndipo ataona Petro anakhala pansi.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 9:40
14 Mawu Ofanana  

Nafuulira kwa Yehova Yesaya mneneriyo, nabweza Iye mthunzi m'mbuyo makwerero khumi, ndiwo amene udatsikira pa makwerero a Ahazi.


Koma iwe popemphera, lowa m'chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.


Koma pamene khamulo linatulutsidwa, Iye analowamo, nagwira dzanja lake; ndipo kabuthuko kadauka.


Ndipo pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lilikuthamangira pamodzi, anadzudzula mzimu woipawo, nanena ndi uwo, Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, Ine ndikulamula iwe, tuluka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye.


Ndipo anapatukana nao kutalika kwake ngati kuponya mwala, nagwada pansi napemphera,


Ndipo Iye anamgwira dzanja lake, naitana, nati, Buthu, tauka.


Ndipo m'mene ananena izi, anagwada pansi, napemphera ndi iwo onse.


Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidachoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana, anatiperekeza kufikira kutuluka m'mzinda; ndipo pogwadira pa mchenga wa kunyanja, tinapemphera,


Ndipo kunatero kuti atate wake wa Publioyo anagona wodwala nthenda ya malungo ndi kamwazi. Kwa iyeyu Paulo analowa, napemphera, naika manja pa iye, namchiritsa.


Ndipo m'mene anagwada pansi, anafuula ndi mau aakulu, Ambuye, musawaikire iwo tchimo ili. Ndipo m'mene adanena ichi, anagona tulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa