Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 9:2 - Buku Lopatulika

2 napempha kwa iye makalata akunka nao ku Damasiko ku masunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 napempha kwa iye akalata akunka nao ku Damasiko ku masunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 kukampempha makalata opita nawo ku nyumba zamapemphero za ku Damasiko. Ankafuna kuti ngati akapezeko ena otsata Njira ya Ambuye, kaya ndi amuna kaya ndi akazi, akaŵamange nkubwera nawo ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 ndi kukapempha makalata a chilolezo kuti apite nawo ku masunagoge a ku Damasiko, kuti ngati atakapezeka ena kumeneko otsata Njirayo, kaya ndi amuna kapena amayi, akawamange ndi kuwatenga kubwera nawo ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 9:2
23 Mawu Ofanana  

Ndipo anadzigawanizira iwo usiku, iye ndi anyamata ake, nawakantha, nawapirikitsa kufikira ku Hoba, ndiko ku dzanja lamanzere la ku Damasiko.


Katundu wa Damasiko. Taonani, Damasiko wachotsedwa usakhalenso mzinda, ndimo udzangokhala muunda wopasulidwa.


Za Damasiko. Hamati ndi Aripadi ali ndi manyazi, chifukwa anamva malodza, asungunuka kunyanja, adera nkhawa osatha kukhala chete.


Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu ku bwalo la akulu a milandu, nadzakukwapulani inu m'masunagoge mwao;


Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.


Iyeyo anaphunzitsidwa m'njira ya Ambuye; pokhala nao mzimu wachangu, ananena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha;


Nthawi yomweyo kunali phokoso lambiri kunena za Njirayo.


Koma pamene ena anaumitsa mtima ndi kusamvera, nanenera zoipa Njirayo pamaso pa anthu, anawachokera, napatutsa ophunzira, nafotokozera masiku onse m'sukulu ya Tirano.


Koma ichi ndivomera kwa inu, kuti monga mwa Njira yonenedwa mpatuko, momwemo nditumikira Mulungu wa makolo athu, ndi kukhulupirira zonse zili monga mwa chilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri;


Koma Felikisi anawalinditsa, popeza anadziwitsadi Njirayo, nati, Pamene Lisiasi kapitao wamkulu akatsika ndidzazindikiritsa konse za kwa inu.


Chimenenso ndinachita mu Yerusalemu: ndipo ndinatsekera ine oyera mtima ambiri m'ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe aakulu; ndiponso pophedwa iwo, ndinavomerezapo.


M'menemo popita ine ku Damasiko ndi ulamuliro ndi ukumu wa kwa ansembe aakulu,


Koma anauka ena a iwo ochokera m'sunagoge wa Alibertino, ndi Akirene, ndi Aaleksandriya, ndi mwa iwo a ku Silisiya ndi ku Asiya, natsutsana ndi Stefano.


Imeneyo inachenjerera fuko lathu, niwachitira choipa makolo athu, niwatayitsa tiana tao, kuti tingakhale ndi moyo.


ndi kuti pano ali nao ulamuliro wa kwa ansembe aakulu wakumanga onse akuitana pa dzina lanu.


Ndipo onse amene anamva anadabwa, nanena, Suyu iye amene anaononga mu Yerusalemu onse akuitana pa dzina ili? Ndipo wadza kuno kudzatero, kuti amuke nao omangidwa kwa ansembe aakulu.


Mu Damasiko kazembe wa mfumu Areta analindizitsa mzinda wa Adamasiko kuti andigwire ine;


kapena kukwera kunka ku Yerusalemu sindinankako kwa iwo amene anakhala atumwi ndisanakhale mtumwi ine, komatu ndinamuka ku Arabiya, ndipo ndinabweranso ku Damasiko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa