Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 8:9 - Buku Lopatulika

9 Koma panali munthu dzina lake Simoni amene adachita matsenga m'mzindamo kale, nadabwitsa anthu a Samariya, ndi kunena kuti iye yekha ndiye munthu wamkulu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Koma panali munthu dzina lake Simoni amene adachita matsenga m'mudzimo kale, nadabwitsa anthu a Samariya, ndi kunena kuti iye yekha ndiye munthu wamkulu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Koma mumzindamo munali munthu wina, dzina lake Simoni amene kale ankachita matsenga, namadodometsa anthu onse a ku Samariyako. Iyeyu ankadzimveketsa kuti ndi munthu wamkulu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Koma mu mzindawo munali munthu dzina lake Simoni, amene amachita za matsenga ndi kudabwitsa anthu a mu Samariya. Iye amadzitamandira kuti ndi wopambana,

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 8:9
20 Mawu Ofanana  

Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aejipito, iwonso anachita momwemo ndi matsenga ao.


Ndipo alembi a Aejipito anachita momwemo ndi matsenga ao; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova.


Ndipo alembi sanathe kuima pamaso pa Mose chifukwa cha zilondazo; popeza panali zilonda pa alembi ndi pa Aejipito onse.


Ndipo munthu wakutembenukira kwa obwebweta ndi anyanga kuwatsata ndi chigololo, nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndipo ndidzamsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake.


Iye wolankhula zochokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha. Iye wakufuna ulemu wa Iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.


Ndipo m'mene anapitirira chisumbu chonse kufikira Pafosi, anapezapo munthu watsenga, mneneri wonyenga, ndiye Myuda, dzina lake Barayesu;


Koma Elimasi watsengayo (pakuti dzina lake litero posandulika) anawakaniza, nayesa kupatutsa kazembe asakhulupirire.


Pakuti asanafike masiku ano anauka Teudasi, nanena kuti ali kanthu iye mwini; amene anthu anaphatikana naye, chiwerengero chao ngati mazana anai; ndiye anaphedwa; ndi onse amene anamvera iye anamwazika, napita pachabe.


Ndipo anamsamalira iye, popeza nthawi yaikulu adawadabwitsa iwo ndi matsenga ake.


amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zotchedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhala pansi ku Kachisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu.


Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika,


akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.


Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, anthu amene adayamba kupulumuka kwa iwo a mayendedwe olakwa;


Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa