Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 8:10 - Buku Lopatulika

10 ameneyo anamsamalira onsewo, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu, ndi kunena, Uyu ndiye mphamvu ya Mulungu, yonenedwa Yaikulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 ameneyo anamsamalira onsewo, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu, ndi kunena, Uyu ndiye mphamvu ya Mulungu, yonenedwa Yaikulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Anthu onse, aang'ono ndi aakulu omwe, ankamumvera namamtsata nkumanena kuti, “Munthu ameneyu ndiye mphamvu ya Mulungu ija amati, Mphamvu yaikulu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 ndipo anthu onse, aakulu ndi aangʼono anamumvera ndi kunena kuti, “Munthu uyu ndi mphamvu ya Mulungu yotchedwa Mphamvu yayikulu.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 8:10
12 Mawu Ofanana  

ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wake, ndi yense mbale wake, kuti, Mudziwe Yehova; pakuti iwo onse adzandidziwa, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu wa iwo, ati Yehova; pakuti ndidzakhululukira mphulupulu yao, ndipo sindidzakumbukira tchimo lao.


Ndipo akazembe onse a nkhondo, ndi Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi Yezaniya mwana wake wa Hosaya, ndi anthu onse kuyambira wamng'ono, kufikira wamkulu, anayandikira,


Pakuti kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu onse akhala akusirira; ndiponso kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita monyenga.


Chifukwa chake ndidzapereka akazi ao kwa ena, ndi minda yao kwa iwo adzalowamo; pakuti onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu asirirasirira; kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita zonyenga.


Ndipo anthu a Ninive anakhulupirira Mulungu, nalalikira chosala, navala chiguduli, kuyambira wamkulu kufikira wamng'ono wa iwowa.


Pamene makamu anaona chimene anachita Paulo, anakweza mau ao, nati m'chinenero cha Likaoniya, Milungu yatsikira kwa ife monga anthu.


Koma anayesa kuti adzatupa, kapena mwini wake kugwa kufa pomwepo; koma m'mene adalindira nthawitu, naona kuti sanapweteke konse, anasintha maganizo, nati, Ndiye Mulungu.


koma kwa iwo oitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Agriki, Khristu mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu.


Pakuti mulolana nao opanda nzeru mokondwera, pokhala anzeru inu nokha.


Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;


Ndipo ambiri adzatsata zonyansa zao; chifukwa cha iwo njira ya choonadi idzanenedwa zamwano.


Ndipo umodzi wa mitu yake unakhala ngati unalasidwa kufikira imfa; ndipo bala lake la kuimfa lidapola; ndipo dziko lonse linazizwa potsata chilombocho;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa