Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 7:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo Stefano anati, Amuna inu, abale, ndi atate, tamverani. Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye mu Mesopotamiya, asanayambe kukhala mu Harani;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Stefano anati, Amuna inu, abale, ndi atate, tamverani. Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye m'Mesopotamiya, asanayambe kukhala m'Harani;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Iye adayankha kuti, “Abale anga ndi atate anga, mverani! Mulungu waulemerero adaonekera kholo lathu Abrahamu pamene ankakhala ku Mesopotamiya, asanakakhale ku Harani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Stefano anayankha kuti, “Abale ndi makolo, tamverani! Mulungu waulemerero anaoneka kwa kholo lathu Abrahamu pamene ankakhala ku Mesopotamiya, asanakakhale ku Harani.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 7:2
29 Mawu Ofanana  

Ndipo Tera anatenga Abramu mwana wake wamwamuna, ndi Loti mwana wa Harani, mwana wake wamwamuna, ndi Sarai mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abramu; ndipo anatuluka pamodzi nao ku Uri wa kwa Akaldeya kuti amuke ku dziko la Kanani, ndipo anafika ku Harani, nakhala kumeneko.


Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Tuluka iwe m'dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi kunyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe;


Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala mu Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.


Ndipo anati kwa iye, Ine ndine Yehova amene ndinatulutsa iwe mu Uri wa kwa Akaldeya, kuti ndikupatse iwe dziko limeneli likhale lakolako.


Ndipo anati Yakobo kwa iwo, Abale anga, ndinu a kuti inu? Nati, Ndife a ku Harani.


Inu ndinu Yehova Mulungu amene munasankha Abramu ndi kumtulutsa mu Uri wa kwa Akaldeya, ndi kumutcha dzina lake Abrahamu;


Mfumu imene ya ulemerero ndani? Yehova wa makamumakamu, ndiye Mfumu ya ulemerero.


Weramutsani mitu yanu, zipata inu; ndipo kwezekani inu, zitseko zosatha, kuti Mfumu ya ulemerero ilowe.


Liu la Yehova lili pamadzi; Mulungu wa ulemerero agunda, ndiye Yehova pamadzi ambiri.


Kodi milungu ya amitundu yaipulumutsa iyo, imene atate anga anaipasula? Gozani ndi Harani ndi Rezefe ndi ana a Edeni amene anali mu Telasara.


Yang'anani kwa Abrahamu kholo lanu, ndi kwa Sara amene anakubalani inu; pakuti pamene iye anali mmodzi yekha ndinamuitana iye; ndipo ndinamdalitsa ndi kumchulukitsa.


Ndipo wina anafuula kwa mnzake, nati, Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake.


Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.


Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.


Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.


Izi anati Yesaya, chifukwa anaona ulemerero wake; nalankhula za Iye.


Amuna, abale, ndi atate, mverani chodzikanira changa tsopano, cha kwa inu.


Ndipo pamene adatero, kunakhala chilekano pakati pa Afarisi ndi Asaduki; ndipo osonkhanawo anagawikana.


Ndipo mkulu wa ansembe anati, Zitero izi kodi?


imene saidziwa mmodzi wa akulu a nthawi ya pansi pano: pakuti akadadziwa sakadapachika Mbuye wa ulemerero;


kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa vumbulutso kuti mukamzindikire Iye;


akulindira chiyembekezo chodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu;


ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu mu Mwamba,


Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako.


Abale anga, pakuti muli nacho chikhulupiriro cha Ambuye wathu Yesu Khristu, Ambuye wa ulemerero, musakhale okondera ndi kusamala maonekedwe.


Ndipo Yoswa ananena ndi anthu onse, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kale lija makolo anu anakhala tsidya lija la mtsinje, ndiye Tera, atate wa Abrahamu ndi atate wa Nahori; natumikira milungu ina iwowa.


Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, ndipo zinalengedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa