Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 6:9 - Buku Lopatulika

9 Koma anauka ena a iwo ochokera m'sunagoge wa Alibertino, ndi Akirene, ndi Aaleksandriya, ndi mwa iwo a ku Silisiya ndi ku Asiya, natsutsana ndi Stefano.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Koma anauka ena a iwo ochokera m'sunagoge wa Alibertino, ndi Akirene, ndi Aaleksandriya, ndi mwa iwo a ku Silisiya ndi ku Asiya, natsutsana ndi Stefano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Koma kudabwera anthu ena a ku Kirene ndi a ku Aleksandriya, a ku nyumba yamapemphero yotchedwa “Nyumba Yamapemphero ya Opatsidwa Ufulu.” Iwoŵa pamodzi ndi ena a ku Silisiya ndi a ku Asiya adayamba kutsutsana ndi Stefano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Panauka mtsutso kuchokera kwa anthu a ku Kurene ndi a ku Alekisandriya komanso a ku dera la Silisiya ndi Asiya, otchedwa a Sunagoge ya Mfulu. Anthu amenewa anayamba kutsutsana ndi Stefano.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 6:9
27 Mawu Ofanana  

Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu ku bwalo la akulu a milandu, nadzakukwapulani inu m'masunagoge mwao;


Chifukwa cha icho, onani, ndituma kwa inu aneneri ndi anzeru ndi alembi; ena a iwo mudzawapha, mudzawapachika; ndi ena a iwo mudzawakwapula m'masunagoge mwanu, ndi kuwazunza, kuchokera kumudzi umodzi, kufikira kumudzi wina;


Ndipo pakutuluka pao anapeza munthu wa ku Kirene, dzina lake Simoni, namkakamiza iye kuti anyamule mtanda wake.


Koma inu mudziyang'anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu ku bwalo la akulu a milandu; ndipo adzakukwapulani m'masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafumu mudzaimirira chifukwa cha Ine, kukhale umboni kwa iwo.


Koma zisanachitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, chifukwa cha dzina langa.


Koma panali ena mwa iwo, amuna a ku Kipro, ndi Kirene, amenewo, m'mene adafika ku Antiokeya, analankhula ndi Agriki, ndi kulalikira Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu.


Ndipo kunali aneneri ndi aphunzitsi ku Antiokeya mu Mpingo wa komweko, ndiwo Barnabasi, ndi Simeoni, wonenedwa Wakuda, ndi Lusio wa ku Kirene, Manaene woleredwa pamodzi ndi Herode chiwangacho, ndi Saulo.


Koma Ayuda, pakuona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zolankhulidwa ndi Paulo, nachita mwano.


Atumwi ndi abale aakulu, kwa abale a mwa amitundu a mu Antiokeya, ndi Siriya, ndi Silisiya, tikupatsani moni:


Ndipo iye anapita kupyola pa Siriya ndi Silisiya, nakhazikitsa Mipingo.


Ndipo anapita padziko la Frijiya ndi Galatiya, atawaletsa Mzimu Woyera kuti asalalikire mau mu Asiya;


Ndipo anafika ku Efeso Myuda wina dzina lake Apolo, fuko lake la ku Aleksandriya, munthu wolankhula mwanzeru; ndipo anali wamphamvu m'malembo.


Ndipo anachita chomwecho zaka ziwiri; kotero kuti onse akukhala mu Asiya anamva mau a Ambuye, Ayuda ndi Agriki.


Ndipo muona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, Si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja:


Ndipo pamene masiku asanu ndi awiri anati amalizidwe, Ayuda a ku Asiya pomuona iye mu Kachisi, anautsa khamu lonse la anthu, namgwira,


Koma Paulo anati, Ine ndine munthu Myuda, wa ku Tariso wa mu Silisiya, mfulu ya mzinda womveka; ndipo ndikupemphani mundilole ndilankhule ndi anthu.


Ndipo ndinati ine, Ambuye, adziwa iwo okha kuti ndinali kuika m'ndende ndi kuwapanda m'masunagoge onse iwo akukhulupirira Inu;


Ine ndine munthu Myuda, wobadwa mu Tariso wa Silisiya, koma ndaleredwa m'mzinda muno, pa mapazi a Gamaliele, wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, ndipo ndinali wachangu, cholinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero;


Ndipo m'mene adawerenga anafunsa achokera m'dziko liti; ndipo pozindikira kuti anali wa ku Silisiya,


popereka izi anandipeza woyeretsedwa mu Kachisi, wopanda khamu la anthu, kapena phokoso;


Ndipo ndinawalanga kawirikawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukulu pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira kumizinda yakunja.


Ndipo sanathe kuipambana nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye.


Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthawi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitse nzeru ya dziko lapansi?


Pamene ndinadza kumbali za Siriya ndi Silisiya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa