Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 4:16 - Buku Lopatulika

16 kuti, Tidzawachitira chiyani anthu awa? Pakutitu chaoneka kwa onse akukhala mu Yerusalemu kuti chizindikiro chozindikirika chachitidwa ndi iwo, ndipo sitingathe kukana.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 kuti, Tidzawachitira chiyani anthu awa? Pakutitu chaoneka kwa onse akukhala m'Yerusalemu kuti chizindikiro chozindikirika chachitidwa ndi iwo, ndipo sitingathe kukana.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Adati, “Kodi tiŵachite chiyani anthu ameneŵa? Pajatu anthu onse okhala m'Yerusalemu muno akudziŵa kuti iwoŵa adachitadi chizindikiro chozizwitsa, ndipo ife zimenezo sitingathe kukana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Iwo anafunsana kuti, “Kodi anthuwa tichite nawo chiyani? Pakuti aliyense okhala mu Yerusalemu akudziwa kuti achita chodabwitsachi, ndipo ife sitingathe kukana.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 4:16
10 Mawu Ofanana  

Ndipo polingirirapo ine, taonani, wadza tonde wochokera kumadzulo, pa nkhope ya dziko lonse lapansi, wosakhudza nthaka; ndi mbuziyo inali ndi nyanga yooneka bwino pakati pamaso ake.


Ndipo tondeyo anadzikulitsa kwakukulu, koma atakhala wamphamvu, nyanga yake yaikulu inathyoka; ndi m'malo mwake munaphuka nyanga zinai zooneka bwino, zoloza kumphepo zinai za mlengalenga.


Iwo ananena kwa iye, Chifukwa palibe munthu anatilemba. Iye anati kwa iwo, Pitani inunso kumundawo wampesa.


Ndipo pa nthawi yomweyo anali ndi wandende wodziwika, dzina lake Barabasi.


Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.


Chifukwa cha ichinso khamulo linadza kudzakomana ndi Iye, chifukwa anamva kuti Iye adachita chizindikiro ichi.


Ndipo sanathe kuipambana nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa