Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 26:9 - Buku Lopatulika

9 Inedi ndinayesa ndekha, kuti kundiyenera kuchita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu Mnazarayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Inedi ndinayesa ndekha, kuti kundiyenera kuchita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu Mnazarayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Ine ndemwe ndinkaganiza kuti ndinkayenera kuchita zinthu zambiri pofuna kuthetsa mbiri ya Yesu wa ku Nazarete.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “Inenso ndimaganiza kuti ndimayenera kuchita zinthu zambiri pofuna kuthana ndi dzina la Yesu wa ku Nazareti.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 26:9
16 Mawu Ofanana  

Koma izi zonse adzakuchitirani chifukwa cha dzina langa, chifukwa sadziwa wondituma Ine.


Pamenepo Paulo anayankha, Muchitanji, polira ndi kundiswera mtima? Pakuti ndakonzeka ine si kumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.


Ine ndine munthu Myuda, wobadwa mu Tariso wa Silisiya, koma ndaleredwa m'mzinda muno, pa mapazi a Gamaliele, wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, ndipo ndinali wachangu, cholinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero;


ndipo ndinalondalonda Njira iyi kufikira imfa, ndi kumanga ndi kupereka kundende amuna ndi akazi.


Ndipo ndinayankha, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati kwa ine, Ndine Yesu wa ku Nazarete, amene umlondalonda.


Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m'dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene;


Ndipo tsopano, abale, ndidziwa kuti munachichita mosadziwa, monganso akulu anu.


Koma Petro anati, Siliva ndi golide ndilibe; koma chimene ndili nacho, ichi ndikupatsa, M'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, yenda.


Koma Saulo, wosaleka kupumira pa ophunzira a Ambuye kuopsa ndi kupha, ananka kwa mkulu wa ansembe,


pakuti Ine ndidzamuonetsa iye zinthu zambiri ayenera iye kuzimva kuwawa chifukwa cha dzina langa.


Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziwitso.


monga mwa changu, wolondalonda Mpingo; monga mwa chilungamo cha m'lamulo wokhala wosalakwa ine.


ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe; komatu anandichitira chifundo, popeza ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira;


Pamenepo amuna akumudziwo anati kwa Yowasi, Umtulutse mwana wako kuti afe; pakuti anagamula guwa la nsembe la Baala, pakutinso analikha chifanizo chinali pomwepo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa