Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 26:10 - Buku Lopatulika

10 Chimenenso ndinachita mu Yerusalemu: ndipo ndinatsekera ine oyera mtima ambiri m'ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe aakulu; ndiponso pophedwa iwo, ndinavomerezapo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Chimenenso ndinachita m'Yerusalemu: ndipo ndinatsekera ine oyera mtima ambiri m'ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe aakulu; ndiponso pophedwa iwo, ndinavomerezapo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ndipo ndidaazichitadi ku Yerusalemu. Akulu a ansembe atandipatsa ulamuliro, ine ndinkaŵatsekera m'ndende anthu ambiri a Mulungu. Pamene iwo ankaphedwa, ine ndinkavomereza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ndipo izi ndi zimene ndinazichita ku Yerusalemu. Ndi ulamuliro wa akulu a ansembe, ine ndinayika mʼndende oyera mtima ambiri, ndipo pamene amaphedwa, ine ndimavomereza.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 26:10
17 Mawu Ofanana  

Za oyera mtima okhala padziko lapansi, iwo ndiwo omveka mbiri, mwa iwowo muli chikondwero changa chonse.


ndipo anamtaya kunja kwa mzinda, namponya miyala; ndipo mbonizo zinaika zovala zao pa mapazi a mnyamata dzina lake Saulo.


Ndipo Saulo analikuvomerezana nao pa imfa yake. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukulu pa Mpingo unali mu Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m'maiko a Yudeya ndi Samariya, koma osati atumwi ai.


Ndipo Saulo anapasula Mpingo, nalowa nyumba ndi nyumba, nakokamo amuna ndi akazi, nawaika m'ndende.


Ndipo onse amene anamva anadabwa, nanena, Suyu iye amene anaononga mu Yerusalemu onse akuitana pa dzina ili? Ndipo wadza kuno kudzatero, kuti amuke nao omangidwa kwa ansembe aakulu.


Koma m'mene anafika ku Yerusalemu, anayesa kudziphatika kwa ophunzira; ndipo anamuopa iye onse, osakhulupirira kuti ali wophunzira.


Koma kunali, pakupita Petro ponseponse, anatsikiranso kwa oyera mtima akukhala ku Lida.


Ndipo Petro anamgwira dzanja, namnyamutsa; ndipo m'mene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo.


Pakuti ine ndili wamng'ono wa atumwi, ndine wosayenera kutchedwa mtumwi, popeza ndinalondalonda Mpingo wa Mulungu.


Pakuti mudamva za makhalidwe anga kale mwa Chiyuda, kuti ndinalondalonda Mpingo wa Mulungu koposa, ndi kuupasula,


Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, kwa oyera mtima amene ali mu Efeso, ndi kwa iwo okhulupirika mwa Khristu Yesu:


Ndipo ndinaona mkazi woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu; ndipo ndinazizwa pakumuona iye ndi kuzizwa kwakukulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa