Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 26:3 - Buku Lopatulika

3 makamaka popeza mudziwitsa miyambo yonse ndi mafunso onse a mwa Ayuda; chifukwa chake ndikupemphani mundimvere ine moleza mtima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 makamaka popeza mudziwitsa miyambo yonse ndi mafunso onse a mwa Ayuda; chifukwa chake ndikupemphani mundimvere ine moleza mtima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Makamaka chifukwa inu mumaidziŵa bwino miyambo yonse yachiyuda, ndiponso mikangano yao yonse, ndikukupemphani kuti mundimvere moleza mtima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 ndipo makamaka chifukwa inu mukudziwa bwino miyambo yonse ya Chiyuda ndiponso zonse zimene amatsutsana. Nʼchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundimvetsere moleza mtima.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 26:3
13 Mawu Ofanana  

Ndipo ndinatenga kalata yogulira, yina yosindikizidwa, monga mwa lamulo ndi mwambo, ndi yina yovundukuka;


ndipo anamva za iwe, kuti uphunzitsa Ayuda onse a kwa amitundu apatukane naye Mose, ndi kuti asadule ana ao, kapena asayende monga mwa miyambo.


Ndipo pamene kazembe anamkodola kuti anene, Paulo anayankha, Podziwa ine kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu zaka zambiri, ndidzikanira mokondwera;


Koma kuti ndingaonjeze kukulemetsani ndikupemphani mutimvere mwachidule ndi chifatso chanu.


Koma ndilibe ine kanthu koti ndinenetse za iye kakulembera kwa mbuye wanga. Chifukwa chake ndamtulutsira kwa inu, ndipo makamaka kwa inu, Mfumu Agripa, kuti, ndikatha kumfunsafunsa, ndikhale nako kanthu kakulembera.


Ndidziyesera wamwai, Mfumu Agripa, popeza nditi ndidzikanira lero pamaso panu, za zonse zimene Ayuda andinenera nazo;


Pakuti mfumuyo idziwa izi, kwa iye imene ndilankhula nayonso mosaopa: pakuti ndidziwadi kuti kulibe kanthu ka izi kadambisikira; pakuti ichi sichinachitike m'tseri.


kufikira komweko mafuko athu khumi ndi awiri, potumikira Mulungu kosapumula usiku ndi usana, ayembekeza kufikirako. Chifukwa cha chiyembekezo ichi, Mfumu, andinenera Ayuda.


Ndipo kunali, atapita masiku atatu, anaitana akulu a Ayuda asonkhane; ndipo atasonkhana, ananena nao, Ine, amuna, abale, ndingakhale sindinachite kanthu kakuipsa anthu, kapena miyambo ya makolo, anandipereka wam'nsinga kuchokera ku Yerusalemu ku manja a Aroma;


pakuti tinamumva iye alikunena, kuti, Yesu Mnazarayo amene adzaononga malo ano, nadzasanduliza miyambo imene Mose anatipatsa.


Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.


Ndipo kudzali, pakukhala iye pa mpando wachifumu wa ufumu wake, adzilemberere chofanana cha chilamulo ichi m'buku, achitenge pa ichi chili pamaso pa ansembe Alevi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa