Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 26:2 - Buku Lopatulika

2 Ndidziyesera wamwai, Mfumu Agripa, popeza nditi ndidzikanira lero pamaso panu, za zonse zimene Ayuda andinenera nazo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndidziyesera wamwai, Mfumu Agripa, popeza nditi ndidzikanira lero pamaso panu, za zonse zimene Ayuda andinenera nazo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Inu Mfumu Agripa, ine ndikuganiza kuti ndine wamwai kuti ndi pamaso panu pamene ndiyankhe lero zonse zimene Ayuda akhala akundineneza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Mfumu Agripa ine ndikudziyesa wa mwayi kuyima pamaso panu lero lino ndi kudziteteza, kutsutsa zonse zimene Ayuda andinenera,

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 26:2
10 Mawu Ofanana  

Ndidzalankhulanso za umboni wanu pamaso pa mafumu, osachitapo manyazi.


Koma pamene paliponse angakuperekeni inu, musamadera nkhawa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene chiyani; pakuti chimene mudzachilankhula, chidzapatsidwa kwa inu nthawi yomweyo;


Ndipo pamene paliponse adzamuka nanu kumlandu wa m'sunagoge ndi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena chiyani;


Koma zisanachitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, chifukwa cha dzina langa.


Koma ndilibe ine kanthu koti ndinenetse za iye kakulembera kwa mbuye wanga. Chifukwa chake ndamtulutsira kwa inu, ndipo makamaka kwa inu, Mfumu Agripa, kuti, ndikatha kumfunsafunsa, ndikhale nako kanthu kakulembera.


Ndipo Agripa anati kwa Paulo, Kwaloleka udzinenere wekha. Pamenepo Paulo, anatambasula dzanja nadzikanira:


Potero, Mfumu Agripa, sindinakhale ine wosamvera masomphenya a Kumwamba;


Pakuti mfumuyo idziwa izi, kwa iye imene ndilankhula nayonso mosaopa: pakuti ndidziwadi kuti kulibe kanthu ka izi kadambisikira; pakuti ichi sichinachitike m'tseri.


makamaka popeza mudziwitsa miyambo yonse ndi mafunso onse a mwa Ayuda; chifukwa chake ndikupemphani mundimvere ine moleza mtima.


kufikira komweko mafuko athu khumi ndi awiri, potumikira Mulungu kosapumula usiku ndi usana, ayembekeza kufikirako. Chifukwa cha chiyembekezo ichi, Mfumu, andinenera Ayuda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa