Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 23:3 - Buku Lopatulika

3 Pamenepo Paulo anati kwa iye, Mulungu adzakupanda iwe, khoma loyeretsedwa iwe; ndipo kodi ukhala iwe wakundiweruza mlandu monga mwa chilamulo, ndipo ulamulira andipande ine posanga chilamulo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pamenepo Paulo anati kwa iye, Mulungu adzakupanda iwe, khoma loyeretsedwa iwe; ndipo kodi ukhala iwe wakundiweruza mlandu monga mwa chilamulo, ndipo ulamulira andipande ine posanga chilamulo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Pamenepo Paulo adamuuza kuti, “Mulungu adzatchaya iweyo, chipupa chopaka njeresawe! Iwe wakhala pamenepo kuti undiweruze potsata Malamulo a Mose, nanga bwanji ukuŵaphwanya Malamulowo pakulamula kuti anditchaye?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pamenepo Paulo anamuwuza kuti, “Mulungu adzakukantha, iwe munthu wachiphamaso! Wakhala pamenepo kuti undiweruze ine monga mwalamulo, koma iweyo ukuphwanya lamulolo polamulira kuti andimenye!”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 23:3
14 Mawu Ofanana  

Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anasendera, napanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandichokera bwanji, kulankhula ndi iwe?


Kodi uyenera kuyanjana ndi Inu mpando wachifumu wa kusakaza, wakupanga chovuta chikhale lamulo?


Ndiponso ndinaona kunja kuno malo akuweruza, komweko kuli zoipa; ndi malo a chilungamo, komweko kuli zoipa.


Musamachita chisalungamo pakuweruza mlandu; usamavomereza munthu wosauka, kapena kulemekeza munthu womveka; uweruze mlandu wa munthu mnzako molungama.


Musamachita chisalungamo poweruza mlandu, poyesa utali wake, kulemera kwake, kapena kuchuluka kwake.


inu osintha chiweruzo chikhale chivumulo, nimugwetsa pansi chilungamo.


Koma Anasi adamtumiza Iye womangidwa kwa Kayafa mkulu wa ansembe.


Kodi chilamulo chathu chiweruza munthu, osayamba kumva iye, ndi kuzindikira chimene achita?


Ndipo iwo akuimirirako anati, Ulalatira kodi mkulu wa ansembe wa Mulungu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa