Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 22:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo kunali, pakupita ine ndi kuyandikira ku Damasiko, monga usana, mwadzidzidzi kunandiwalira pondizungulira ine kuunika kwakukulu kochokera kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo kunali, pakupita ine ndi kuyandikira ku Damasiko, monga usana, mwadzidzidzi kunandiwalira pondizungulira ine kuunika kwakukulu kochokera kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 “Pamene ndinali pa ulendowo ndi kuyandikira Damasiko, nthaŵi ili ngati 12 koloko yamasana, mwadzidzidzi kuŵala kwakukulu kochokera kumwamba kudandizinga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 “Nthawi ya masana, nditayandikira ku Damasiko, mwadzidzidzi kuwala kwakukulu kochokera kumwamba kunandizungulira.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 22:6
11 Mawu Ofanana  

Ndipo anadzigawanizira iwo usiku, iye ndi anyamata ake, nawakantha, nawapirikitsa kufikira ku Hoba, ndiko ku dzanja lamanzere la ku Damasiko.


Ndipo Abramu anati, Ambuye Mulungu, mudzandipatsa ine chiyani popeza ndine wopanda mwana, ndi amene adzakhala mwini nyumba yanga ndiye Eliyezere wa ku Damasiko?


Pamenepo Davide anaika maboma mu Aramu wa Damasiko. Ndipo Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Ndipo Yehova anamsunga Davide kulikonse anamukako.


Pompo mwezi udzanyazitsidwa, ndi dzuwa lidzakhala ndi manyazi, pakuti Yehova wa makamu adzalamulira chaulemerero m'phiri la Ziyoni, ndi mu Yerusalemu, ndi pamaso pa akuluakulu ake.


ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yake inawala monga dzuwa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbuu monga kuwala.


Ndipo ndinagwa pansitu, ndipo ndinamva mau akunena nane, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine?


Ndipo chidauka chipolowe chachikulu, ndipo alembi ena a kwa Afarisi anaimirira, natsutsana, nanena, Sitipeza choipa chilichonse mwa munthuyu; ndipo nanga bwanji ngati mzimu kapena mngelo walankhula naye?


ndipo potsiriza pake pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo.


Ndipo m'dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndi m'kamwa mwake mudatuluka lupanga lakuthwa konsekonse; ndipo nkhope yake ngati dzuwa lowala mu mphamvu yake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa