Machitidwe a Atumwi 22:5 - Buku Lopatulika5 Monganso mkulu wa ansembe andichitira umboni, ndi bwalo lonse la akulu; kwa iwo amenenso ndinalandira makalata kunka nao kwa abale, ndipo ndinapita ku Damasiko, kuti ndikatenge iwonso akukhala kumeneko kudza nao omangidwa ku Yerusalemu, kuti alangidwe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Monganso mkulu wa ansembe andichitira umboni, ndi bwalo lonse la akulu; kwa iwo amenenso ndinalandira akalata kunka nao kwa abale, ndipo ndinapita ku Damasiko, kuti ndikatenge iwonso akukhala kumeneko kudza nao omangidwa ku Yerusalemu, kuti alangidwe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Mkulu wa ansembe onse ndi onse a m'Bungwe la akuluakulu a Ayuda angathe kundivomereza. Iwowo adaandipatsa makalata opita nawo kwa abale athu achiyuda ku Damasiko. Tsono ndidapita komweko kuti ndikaŵagwire anthu ameneŵa, ndi kubwera nawo ku Yerusalemu ali omangidwa, kuti adzalangidwe.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Mkulu wa ansembe ndiponso akuluakulu a Ayuda angathe kundichitira umboni. Iwowa anandipatsa makalata opita nawo kwa abale awo ku Damasiko. Ndipo ndinapita kumeneko kuti ndikawagwire anthu amenewa ndi kubwera nawo ku Yerusalemu kuti adzalangidwe. Onani mutuwo |