Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 20:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo mnyamata dzina lake Yutiko anakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikulu; ndipo pakukhala chifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo, anagwa posanja pachiwiri, ndipo anamtola wakufa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo mnyamata dzina lake Yutiko anakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikulu; ndipo pakukhala chifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo, anagwa posanja pachiwiri, ndipo anamtola wakufa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Mnyamata wina, dzina lake Yutiko, adaakhala pa windo. Tsono Paulo akukambabe ndi anthu aja, Yutikoyo ankaodzera kwambiri, mpaka adagona tulo ndithu, nagwa pansi kuchokera pa nyumba yam'mwamba. Ndipo adamtola ali wakufa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Pa chipinda chachitatu chammwamba cha nyumbayo, pa zenera, panakhala mnyamata wina dzina lake Utiko, amene ankasinza pomwe Paulo amayankhulabe. Atagona tulo, iye anagwa pansi kuchokera pa chipinda chammwamba ndipo anamutola atafa.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 20:9
9 Mawu Ofanana  

Ndipo ananena naye, Ndipatse mwana wako. Namtenga m'mfukato mwake napita naye ku chipinda chosanja chogonamo iyeyo, namgoneka pa kama wa iye mwini.


kuti angabwere balamanthu nakakupezani muli m'tulo.


Ndipo pamene unafuula, numng'ambitsa, unatuluka; ndipo mwana anakhala ngati wakufa; kotero kuti ambiri ananena, Wamwalira.


Ndipo anafika kumeneko Ayuda kuchokera ku Antiokeya ndi Ikonio; nakopa makamu, ndipo anamponya Paulo miyala, namguzira kunja kwa mzinda; namuyesa kuti wafa.


Ndipo potsikirako Paulo, anamgwera namfungatira, nati, Musachite phokoso, pakuti moyo wake ulipo.


Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati achoke m'mawa mwake; ndipo ananena chinenere kufikira pakati pa usiku.


Ndipo munali nyali zambiri m'chipinda chapamwamba m'mene tinasonkhanamo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa