Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 19:2 - Buku Lopatulika

2 ndipo anati kwa iwo, Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira? Ndipo anati, Iai, sitinamve konse kuti Mzimu Woyera waperekedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 ndipo anati kwa iwo, Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira? Ndipo anati, Iai, sitinamva konse kuti Mzimu Woyera waperekedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 ndipo adaŵafunsa kuti, “Kodi mudalandira Mzimu Woyera pamene mudakhulupirira?” Iwo adati, “Nkumva komwe sitinamve kuti kuli Mzimu Woyera.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iye anawafunsa kuti, “Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira?” Iwo anayankha kuti, “Ayi, ife sitinamvepo kuti kuli Mzimu Woyera.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 19:2
12 Mawu Ofanana  

Koma ichi anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, chifukwa Yesu sanalemekezedwe panthawi pomwepo.


Petro ali chilankhulire, Mzimu Woyera anagwa pa onse akumva mauwo.


Pamene anamva ichi, anabatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu.


Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse, ndipo ana anu aamuna, ndi aakazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto;


Pakuti ndilakalaka kuonana ndinu, kuti ndikagawire kwa inu mtulo wina wauzimu, kuti inu mukhazikike;


Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.


Ndipo iye amene akuonjezerani inu Mzimuyo, nachita zimphamvu mwa inu, atero kodi ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro?


Koma Samuele sanadziwe Yehova, ndiponso mau a Yehova sanaululidwe kwa iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa