Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 19:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo panali, pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo anapita pa maiko a pamtunda, nafika ku Efeso, napeza ophunzira ena;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo panali, pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo anapita pa maiko a pamtunda, nafika ku Efeso, napeza ophunzira ena;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo adayendera maiko apamtunda, nakafika ku Efeso. Kumeneko adapezako ophunzira ena,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Apolo ali ku Korinto, Paulo anadutsa mʼmayiko a ku mtunda ndipo anafika ku Efeso. Kumeneko anapeza ophunzira ena.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 19:1
16 Mawu Ofanana  

Zitapita izi anachoka ku Atene, nadza ku Korinto.


Ndipo Krispo, mkulu wa sunagoge, anakhulupirira Ambuye, ndi apabanja ake onse; ndipo Akorinto ambiri anamva, nakhulupirira, nabatizidwa.


Zimenezo zidamveka kwa onse, Ayuda ndi Agriki, amene anakhala ku Efeso; ndipo mantha anagwera onsewo, ndipo dzina la Ambuye Yesu linakuzika.


Ndipo muona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, Si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja:


Pakuti Paulo adatsimikiza mtima apitirire pa Efeso, angataye nthawi mu Asiya; pakuti anafulumira, ngati kutheka, akhale ku Yerusalemu tsiku la Pentekoste.


Ndipo pamene anafika kuli iye, anati kwa iwo, Mudziwa inu kuyambira tsiku loyamba ndinafika ku Asiya, makhalidwe anga pamodzi ndi inu nthawi yonse,


Pakuti adaona Trofimo wa ku Efeso kale pamodzi ndi iye mumzinda; ameneyo anayesa kuti Paulo anamtenga nalowa naye ku Kachisi.


Koma ichi ndinena, kuti yense wa inu anena, Ine ndine wa Paulo; koma ine wa Apolo; koma ine wa Kefa; koma ine wa Khristu.


Ngati ndinalimbana ndi zilombo ku Efeso monga mwa munthu, ndipindulanji? Ngati akufa saukitsidwa, tidye timwe pakuti mawa timwalira.


Koma za Apolo, mbaleyo, ndamuumiriza iye, adze kwa inu pamodzi ndi abale; ndipo sichinali chifuniro chake kuti adze tsopano, koma adzafika pamene aona nthawi.


Koma ndidzakhala ku Efeso kufikira Pentekoste.


Koma izi, abale, ndadziphiphiritsira ndekha ndi Apolo, chifukwa cha inu, kuti mwa ife mukaphunzire kusapitirira zimene zilembedwa; kuti pasakhale mmodzi wodzitukumulira mnzake ndi kukana wina.


Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, kwa oyera mtima amene ali mu Efeso, ndi kwa iwo okhulupirika mwa Khristu Yesu:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa