Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 18:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo anafotokozera m'sunagoge masabata onse, nakopa Ayuda ndi Agriki.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo anafotokozera m'sunagoge masabata onse, nakopa Ayuda ndi Agriki.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Pa tsiku la Sabata lililonse iye ankakambirana ndi anthu ku nyumba yamapemphero ya Ayuda, namayesetsa kukopa Ayuda ndi Agriki omwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Tsiku la Sabata lililonse Paulo amakambirana ndi anthu mʼsunagoge, kufuna kukopa Ayuda ndi Agriki.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 18:4
18 Mawu Ofanana  

Mulungu akuze Yafeti, akhale iye m'mahema a Semu; Kanani akhale kapolo wake.


Sakukopani Hezekiya, kuti akuperekeni mufe nayo njala ndi ludzu, ndi kuti, Yehova Mulungu wathu adzatilanditsa m'dzanja la mfumu ya Asiriya?


Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.


Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analowa m'sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m'kalata.


Chifukwa chake Ayuda anati mwa iwo okha, Adzanka kuti uyu kuti ife sitikampeza Iye? Kodi adzamuka kwa Agriki obalalikawo, ndi kuphunzitsa Agriki?


Koma iwowa, atapita pochokera ku Perga anafika ku Antiokeya wa mu Pisidiya; ndipo analowa m'sunagoge tsiku la Sabata, nakhala pansi.


Ndipo kunali pa Ikonio kuti analowa pamodzi m'sunagoge wa Ayuda, nalankhula kotero, kuti khamu lalikulu la Ayuda ndi Agriki anakhulupirira.


Amenewa anali mfulu koposa a mu Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m'malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.


Chotero tsono anatsutsana ndi Ayuda ndi akupembedza m'sunagoge, ndi m'bwalo la malonda masiku onse ndi iwo amene anakomana nao.


kuti, Uyu akopa anthu apembedze Mulungu pokana chilamulo.


Ndipo iwo anafika ku Efeso, ndipo iye analekana nao pamenepo: koma iye yekha analowa m'sunagoge, natsutsana ndi Ayuda.


Ndipo muona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, Si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja:


Ndipo iye analowa m'sunagoge, nanena molimba mtima, miyezi itatu, natsutsana ndi kukopa kunena za Ufumu wa Mulungu.


Ndipo Agripa anati kwa Paulo, Ndi kundikopa pang'ono ufuna kundiyesera Mkhristu.


Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m'chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.


Ndipo pomwepo m'masunagoge analalikira Yesu, kuti Iye ndiye Mwana wa Mulungu.


Podziwa tsono kuopsa kwa Ambuye, tikopa anthu, koma tionetsedwa kwa Mulungu; ndipo ndiyembekezanso kuti tionetsedwa m'zikumbu mtima zanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa