Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 18:5 - Buku Lopatulika

5 Koma pamene Silasi ndi Timoteo anadza potsika ku Masedoniya, Paulo anapsinjidwa ndi mau, nachitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Koma pamene Silasi ndi Timoteo anadza potsika ku Masedoniya, Paulo anapsinjidwa ndi mau, nachitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Silasi ndi Timoteo atafika kuchokera ku Masedoniya, Paulo tsopano ankangogwira ntchito yolalikira, ndi kuŵauza Ayuda monenetsa kuti Yesu ndiye anali Mpulumutsi wolonjezedwa uja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Sila ndi Timoteyo atafika kuchokera ku Makedoniya, Paulo ankangogwira ntchito yolalikira yokha basi, kuchitira umboni Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 18:5
33 Mawu Ofanana  

Ndipo ngati nditi, Sindidzamtchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lake, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.


Chifukwa chake ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa misonkhano ya anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, okalamba ndi iye amene achuluka masiku ake.


M'mwemo mzimu unandinyamula ndi kuchoka nane; ndipo ndinamuka wowawidwa, womyuka mtima; koma dzanja la Yehova linandigwirizitsa.


Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi chiweruzo, ndi chamuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwake, ndi kwa Israele tchimo lake.


Koma ndili ndi ubatizo ndikabatizidwe nao; ndipo ndikanikizidwa Ine kufikira ukatsirizidwa!


pakuti ndili nao abale asanu; awachitire umboni iwo kuti iwonso angadze kumalo ano a mazunzo.


Anayamba iye kupeza mbale wake yekha Simoni, nanena naye, Tapeza ife Mesiya (ndiko kusandulika Khristu).


Pamenepo Ayuda anamzungulira Iye, nanena ndi Iye, Kufikira liti musinkhitsasinkhitsa moyo wathu? Ngati Inu ndinu Khristu, tiuzeni momveka.


Ndipo inunso muchita umboni, pakuti muli ndi Ine kuyambira chiyambi.


Inu nokha mundichitira umboni, kuti ndinati, Sindine Khristu, koma kuti ndili wotumidwa m'tsogolo mwake mwa Iye.


Ndipo anatilamulira ife tilalikire kwa anthu, ndipo tichite umboni kuti Uyu ndiye amene aikidwa ndi Mulungu akhale woweruza amoyo ndi akufa.


Pamenepo chinakomera atumwi ndi akulu ndi Mpingo wonse kusankha anthu a m'gulu lao, ndi kuwatumiza ku Antiokeya ndi Paulo ndi Barnabasi; ndiwo Yudasi wotchedwa Barsabasi, ndi Silasi, akulu a mwa abale; ndipo analembera mau natumiza ndi iwo:


Ndipo anafikanso ku Deribe ndi Listara; ndipo taonani, panali wophunzira wina pamenepo, dzina lake Timoteo, amake ndiye Myuda wokhulupirira; koma atate wake ndiye Mgriki.


pochokera kumeneko tinafika ku Filipi, mzinda wa ku Masedoniya, waukulu wa m'dzikomo, wa midzi ya Roma; ndipo tidagona momwemo masiku ena.


Ndipo masomphenya anaonekera kwa Paulo usiku: Panali munthu wa ku Masedoniya alinkuimirira, namdandaulira kuti, Muolokere ku Masedoniya kuno, mudzatithangate ife.


natsimikiza, kuti kunayenera Khristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Khristu.


pakuti ndi mphamvu anatsutsa Ayuda, pamaso pa anthu, nasonyeza mwa malembo kuti Yesu ndiye Khristu.


Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika.


ndi kuchitira umboni Ayuda ndi Agriki wa kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.


koma kuti Mzimu Woyera andichitira umboni m'mizinda yonse, ndi kunena kuti nsinga ndi zisautso zindilindira.


Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.


pakuti sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.


Koma Saulo anakula makamaka mumphamvu, nadodometsa Ayuda akukhala mu Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndi Khristu.


Pakuti Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, amene analalikidwa mwa inu ndi ife, (ine ndi Silivano ndi Timoteo) sanakhale eya ndi iai, koma anakhala eya mwa Iye.


ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindinasaukitse munthu aliyense; pakuti abale akuchokera ku Masedoniya, anakwaniritsa kusowa kwanga; ndipo m'zonse ndinachenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzachenjerapo.


Pakuti chikondi cha Khristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti mmodzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa;


Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala nacho cholakalaka cha kuchoka kukhala ndi Khristu, ndiko kwabwino koposaposatu;


ndipo tinatuma Timoteo, mbale wathuyo ndi mtumiki wa Mulungu mu Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti akhazikitse inu, ndi kutonthoza inu za chikhulupiriro chanu;


Koma tsopano pofika Timoteo kwathu kuchokera kwa inu, ndi kutifotokozera mbiri yokoma ya chikhulupiriro ndi chikondano chanu, ndi kuti mutikumbukira bwino masiku onse, pokhumba kutiona ife, monganso ife kukuonani inu;


Mwa Silivano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwachidule, ndi kudandaulira, ndi kuchita umboni, kuti chisomo choona cha Mulungu ndi ichi; m'chimenechi muimemo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa