Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 12:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo anatuluka, namtsata; ndipo sanadziwe kuti nchoona chochitidwa ndi mngelo, koma anayesa kuti alikuona masomphenya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo anatuluka, namtsata; ndipo sanadziwa kuti nchoona chochitidwa ndi mngelo, koma anayesa kuti alikuona masomphenya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Apo Petro adatuluka namtsata, osazindikira kuti zimene mngelo ankachitazo nzoona. Ankangoyesa kuti akuwona zinthu m'masomphenya chabe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Petro anatsatira natuluka mʼndende, koma sanazindikire kuti zimene mngeloyo amachita zimachitikadi; iye amaganiza kuti amaona masomphenya.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 12:9
12 Mawu Ofanana  

Ndipo anamfotokozera iye kuti, Yosefe akali ndi moyo, ndipo alamulira m'dziko lonse la Ejipito. Pamenepo mtima wake unakomoka, pakuti sanawakhulupirire iwo.


Chotero anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.


Pobweza Yehova ukapolo wa Ziyoni, tinakhala ngati anthu akulota.


Amake ananena kwa atumiki, Chimene chilichonse akanena kwa inu, chitani.


Ndipo pokayikakayika Petro mwa yekha ndi kuti masomphenya adawaona akuti chiyani, taonani, amuna aja otumidwa ndi Kornelio, atafunsira nyumba ya Simoni, anaima pachipata,


Iye anapenya m'masomphenya poyera, mngelo wa Mulungu alinkudza kwa iye, ngati ora lachisanu ndi chinai la usana, nanena naye, Kornelio.


Ndinali ine m'mzinda wa Yopa ndi kupemphera; ndipo m'kukomoka ndinaona masomphenya, chotengera chilikutsika, ngati chinsalu chachikulu chogwiridwa pangodya zake zinai; ndi kutsika kumwamba, ndipo chinadza pali ine;


Ndipo mngelo anati kwa iye, Dzimangire m'chuuno, numange nsapato zako. Nachita chotero. Ndipo ananena naye, Funda chovala chako, nunditsate ine.


Potero, Mfumu Agripa, sindinakhale ine wosamvera masomphenya a Kumwamba;


Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lake Ananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m'masomphenya, Ananiya. Ndipo anati, Ndili pano, Ambuye,


Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa