Machitidwe a Atumwi 12:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo m'mene adapitirira podikira poyamba ndi pachiwiri, anadza kuchitseko chachitsulo chakuyang'ana kumzinda; chimene chidawatsegukira chokha; ndipo anatuluka, napitirira khwalala limodzi; ndipo pomwepo mngelo anamchokera. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo m'mene adapitirira podikira poyamba ndi pachiwiri, anadza kuchitseko chachitsulo chakuyang'ana kumudzi; chimene chidawatsegukira chokha; ndipo anatuluka, napitirira khwalala limodzi; ndipo pomwepo mngelo anamchokera. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Onsewo adapitirira gulu loyamba la asilikali aja, kenaka lachiŵiri, mpaka kukafika pa chitseko chachitsulo cha pa chipata choloŵera mu mzinda. Chitsekocho chidangodzitsekukira chokha, iwowo nkutuluka. Adayenda ndithu mu mseu wina wamumzindamo. Atafika polekezera pake mngelo uja adamchokera. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Iwo anadutsa gulu loyamba ndi lachiwiri la asilikali ndipo anafika pa chitseko chachitsulo cholowera mu mzinda. Chitsekocho chinatsekuka chokha ndipo anadutsa. Pamene anayenda kutalika kwa msewu umodzi, mwadzidzidzi mngelo uja anachoka. Onani mutuwo |