Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 12:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo mngelo anati kwa iye, Dzimangire m'chuuno, numange nsapato zako. Nachita chotero. Ndipo ananena naye, Funda chovala chako, nunditsate ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo mngelo anati kwa iye, Dzimangire m'chuuno, numange nsapato zako. Nachita chotero. Ndipo ananena naye, Funda chovala chako, nunditsate ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Kenaka mngelo uja adamuuza kuti, “Vala lamba wako ndi nsapato zako.” Petro atachita zimenezi mngelo uja adamuuzanso kuti, “Fundira mwinjiro wako, unditsate.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Kenaka mngelo anati kwa iye, “Vala zovala ndi nsapato.” Ndipo Petro atachita izi mngeloyo anamuwuzanso kuti, “Funda chovala chako ndipo unditsate.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 12:8
7 Mawu Ofanana  

Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:


koma avale nsapato; ndipo anati, Musavale malaya awiri.


Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'chuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.


Ndipo taonani, mngelo wa Ambuye anaimirirapo, ndipo kuunika kunawala mokhalamo iye; ndipo anakhoma Petro m'nthiti, namuutsa iye, nanena, Tauka msanga. Ndipo maunyolo anagwa kuchoka m'manja mwake.


Ndipo anatuluka, namtsata; ndipo sanadziwe kuti nchoona chochitidwa ndi mngelo, koma anayesa kuti alikuona masomphenya.


Pakuti anaimirira kwa ine usiku walero mngelo wa Mulungu amene ndili wake, amenenso ndimtumikira,


Koma mngelo wa Ambuye analankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka, nupite mbali ya kumwera, kutsata njira yotsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Gaza; ndiyo ya chipululu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa