Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 10:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo m'mene atachoka mngelo amene adalankhula naye, anaitana anyamata ake awiri, ndi msilikali wopembedza, wa iwo amene amtumikira kosaleka;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo m'mene atachoka mngelo amene adalankhula naye, anaitana anyamata ake awiri, ndi msilikali wopembedza, wa iwo amene amtumikira kosaleka;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Mngelo amene ankalankhula naye uja atachoka, Kornelio adaitana antchito ake aŵiri, ndiponso msilikali. Msilikaliyo anali mmodzi mwa amene ankamutumikira, ndipo anali munthu wopembedza Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Mngeloyo anayankhula naye anachoka, Korneliyo anayitana antchito ake awiri ndiponso msilikali mmodzi wa iwo amene ankamutumikira yemwe ankapembedza Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 10:7
13 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene anamva mauwo mnyamata wa Abrahamu, anamgwadira Yehova pansi.


Ndipo pamene iwo anachoka, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m'kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthawire ku Ejipito, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukaononga Iko.


Ndipo onani, mu Yerusalemu munali munthu, dzina lake Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, analikulindira matonthozedwe a Israele; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye.


Ndipo asilikali omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizichita chiyani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu aliyense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu.


acherezedwa iye ndi wina Simoni wofufuta zikopa, nyumba yake ili m'mbali mwa nyanja.


ndipo m'mene adawafotokozera zonse, anawatuma ku Yopa.


Ndipo iwo akukhala nao ambuye okhulupirira, asawapeputse popeza ali abale; koma makamaka awatumikire popeza ali okhulupirira ndi okondedwa, oyanjana nao pa chokomacho. Izi uphunzitse, nuchenjeze.


osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m'thupi, ndiponso mwa Ambuye.


Koma ngati uopa kutsika, utsike naye Pura mnyamata wako kumisasa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa