Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 1:11 - Buku Lopatulika

11 amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Anthuwo adaŵafunsa kuti, “Inu anthu a ku Galileya, mwatani mwangoti chilili pamenepa mukuyang'ana kumwamba? Yesuyu amene watengedwa kuchokera pakati panu kupita Kumwamba, adzabweranso monga momwe mwamuwoneramu akupita Kumwambako.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Iwo anati, “Inu, anthu a ku Galileya, chifukwa chiyani mukuyima ndi kumayangʼana mʼmitambo? Yesu amene wachotsedwa pakati panu ndi kupita kumwamba, adzabweranso mʼnjira yomweyi mwamuona akupita kumwamba.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 1:11
23 Mawu Ofanana  

Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wake, pamodzi ndi angelo ake; ndipo pomwepo Iye adzabwezera kwa anthu onse monga machitidwe ao.


Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pano sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa Munthu atadza mu ufumu wake.


ndipo pomwepo padzaoneka m'thambo chizindikiro cha Mwana wa Munthu; ndipo mitundu yonse ya padziko lapansi idzadziguguda pachifuwa, nidzapenya Mwana wa Munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.


Koma pamene Mwana wa Munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake:


Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa Munthu alinkudza m'mitambo ndi mphamvu yaikulu, ndi ulemerero.


Koma anakananso. Ndipo patapita kamphindi, akuimirirapo ananenanso ndi Petro, Zedi uli wa awo; pakutinso uli Mgalileya.


Pamenepo Ambuye Yesu, atatha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala padzanja lamanja la Mulungu.


Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa Munthu alinkudza mu mtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.


ndipo m'mene anakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zao, anati kwa iwo, Mufuniranji wamoyo pa akufa?


Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.


kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba, atatha kulamula mwa Mzimu Woyera atumwi amene adawasankha;


kuyambira ubatizo wa Yohane, kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba kutisiya ife, mmodzi wa awa akhale mboni ya kuuka kwake pamodzi ndi ife.


Ndipo m'mene adanena izi, ali chipenyerere iwo, ananyamulidwa; ndipo mtambo unamlandira Iye kumchotsa kumaso kwao.


ndipo anaonekera masiku ambiri ndi iwo amene anamperekeza Iye pokwera ku Yerusalemu kuchokera ku Galileya, amenewo ndiwo akumchitira umboni tsopano kwa anthu.


Ndipo anadabwa onse, nazizwa, nanena, Taonani, awa onse alankhulawa sali Agalileya kodi?


Koma m'mene Petro anachiona, anayankha kwa anthu, Amuna inu a Israele, muzizwa naye bwanji ameneyo? Kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamyendetsa iye ndi mphamvu ya ife eni, kapena ndi chipembedzo chathu?


amene thambo la kumwamba liyenera kumlandira kufikira nthawi zakukonzanso zinthu zonse, zimene Mulungu analankhula za izo m'kamwa mwa aneneri ake oyera chiyambire.


ndi kulindirira Mwana wake achokere Kumwamba, amene anamuukitsa kwa akufa, Yesu, wotipulumutsa ife kumkwiyo ulinkudza.


Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mau a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Khristu adzayamba kuuka;


kotero Khristunso ataperekedwa nsembe kamodzi kukasenza machimo a ambiri, adzaonekera pa nthawi yachiwiri, wopanda uchimo, kwa iwo amene amlindirira, kufikira chipulumutso.


Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso lililonse lidzampenya Iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse a padziko adzamlira Iye. Terotu. Amen.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa