Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 9:52 - Buku Lopatulika

52 natumiza amithenga patsogolo pake; ndipo ananka, nalowa m'mudzi wa Asamariya, kukamkonzera Iye malo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

52 natumiza amithenga patsogolo pake; ndipo ananka, nalowa m'mudzi wa Asamariya, kukamkonzera Iye malo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

52 Motero adatuma amithenga kuti atsogole, akaloŵe m'mudzi wina wa Asamariya kukamkonzera malo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

52 ndipo anatuma nthumwi kuti zitsogole. Iwo anapita mʼmudzi wa Asamariya kuti akonzekere kumulandira,

Onani mutuwo Koperani




Luka 9:52
13 Mawu Ofanana  

Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.


Awa amene, khumi ndi awiriwa, Yesu anawatumiza, nawalangiza ndi kuti, Musapite kunjira ya kwa anthu akunja, ndi m'mudzi wa Asamariya musamalowamo:


Zitapita izi Ambuye anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiriawiri pamaso pake kumudzi uliwonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini.


Koma Msamariya wina ali pa ulendo wake anadza pali iye; ndipo pakumuona, anagwidwa chifundo,


Ndipo kunali, pakumuka ku Yerusalemu Iye analikupita pakati pa Samariya ndi Galileya.


ndipo anagwa nkhope yake pansi kumapazi ake, namyamika Iye; ndipo anali Msamariya ameneyo.


Uyu ndi iye amene kunalembedwa za iye, Ona, ndituma Ine mthenga wanga akutsogolere, amene adzakukonzera njira yako pamaso pako.


Ndipo anayenera kupita pakati pa Samariya.


Chifukwa chake anadza kumzinda wa Samariya, dzina lake Sikari, pafupi pa kadziko kamene Yakobo adapatsa mwana wake Yosefe;


Pamenepo mkazi wa mu Samariya ananena ndi Iye, Bwanji Inu, muli Myuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi Msamariya? (Pakuti Ayuda sayenderana nao Asamariya).


Ayuda anayankha nati kwa Iye, Kodi sitinenetsa kuti Inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiwanda?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa