Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 9:29 - Buku Lopatulika

29 Ndipo m'kupemphera kwake, maonekedwe a nkhope yake anasandulika, ndi chovala chake chinayera ndi kunyezimira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Ndipo m'kupemphera kwake, maonekedwe a nkhope yake anasandulika, ndi chovala chake chinayera ndi kunyezimira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Pamene Iye ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake adasandulika, ndipo zovala zake zidachita kuti mbee kuyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Pamene Iye ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake, ndi zovala zake zinawala monyezimira kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Luka 9:29
17 Mawu Ofanana  

Maso ako adzaona mfumu m'kukongola kwake; iwo adzaona dziko lakutali.


Pakuti ameneyo adzaphuka pamaso pake ngati mtengo wanthete, ndi ngati muzu womera m'nthaka youma; Iye alibe maonekedwe, pena kukongola; ndipo pamene timuona palibe kukongola kuti timkhumbe.


ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yake inawala monga dzuwa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbuu monga kuwala.


Ndipo zitatha izi, anaonekanso Iye m'maonekedwe ena kwa awiri a iwo alikuyenda kupita kumidzi.


Pamene anthu onse anabatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa. Iye anali kupemphera, ndipo kuthambo kunatseguka,


Koma Iye anazemba, nanka m'mapululu, nakapemphera.


Ndipo kunali masiku awa, Iye anatuluka nanka kuphiri kukapemphera; nachezera usiku wonse m'kupemphera kwa Mulungu.


Ndipo kunali, pamene Iye anali kupemphera padera, ophunzira anali naye; ndipo anawafunsa iwo, kuti, Makamuwo a anthu anena kuti Ine ndine yani?


Ndipo onani, analikulankhulana naye amuna awiri, ndiwo Mose ndi Eliya;


Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.


Ndipo anampenyetsetsa onse akukhala m'bwalo la akulu a milandu, naona nkhope yake ngati nkhope ya mngelo.


Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa