Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 9:13 - Buku Lopatulika

13 Koma anati kwa iwo, Muwapatse chakudya ndinu. Koma anati, Ife tilibe mikate, koma isanu yokha, ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Koma anati kwa iwo, Muwapatse kudya ndinu. Koma anati, Ife tilibe mikate, koma isanu yokha, ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Koma Yesu adaŵauza kuti, “Inuyo apatseni chakudya.” Iwo adati, “Tili ndi buledi msanu ndi nsomba ziŵiri zokha. Kaya kapena tipite tikaŵagulire anthu onseŵa chakudya?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Iye anayankha kuti, “Apatseni chakudya kuti adye.” Iwo anayankha kuti, “Ife tili ndi malofu a buledi asanu okha ndi nsomba ziwiri, pokhapokha titapita kukagula chakudya cha gulu la anthu onsewa.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 9:13
8 Mawu Ofanana  

Koma dzuwa lidapendeka; ndipo khumi ndi awiriwo anadza, nati kwa Iye, Tauzani makamu a anthu amuke, kuti apite kumidzi yoyandikira ndi kumadera, kukafuna pogona, ndi kupeza zakudya; chifukwa tili kumalo achipululu kuno.


Pakuti anali amuna ngati zikwi zisanu. Koma Iye anati kwa ophunzira ake, Khalitsani iwo pansi magulumagulu, ngati makumi asanuasanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa