Luka 9:12 - Buku Lopatulika12 Koma dzuwa lidapendeka; ndipo khumi ndi awiriwo anadza, nati kwa Iye, Tauzani makamu a anthu amuke, kuti apite kumidzi yoyandikira ndi kumadera, kukafuna pogona, ndi kupeza zakudya; chifukwa tili kumalo achipululu kuno. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Koma dzuwa lidapendeka; ndipo khumi ndi awiriwo anadza, nati kwa Iye, Tauzani makamu a anthu amuke, kuti apite kumidzi yoyandikira ndi kumilaga, kukafuna pogona, ndi kupeza zakudya; chifukwa tili kumalo achipululu kuno. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Dzuŵa lili pafupi kuloŵa, ophunzira khumi ndi aŵiri aja adadzauza Yesu kuti, “Bwanji anthuŵa azinyamuka tsopano, apite ku midzi ndi ku miraga ili pafupiyi, kuti akapeze malo ogona ndiponso chakudya, chifukwatu kuno nkuthengo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Chakumadzulo dzuwa litapita, khumi ndi awiriwo anabwera kwa Iye ndipo anati, “Uzani gulu la anthuli lichoke kuti apite ku midzi yotizungulira ndi madera a ku mudzi kuti akapeze chakudya ndi pogona, chifukwa kuno ndi kuthengo.” Onani mutuwo |